Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"BWENZI TIKUTI BLUE EAGLES YAPEZA 3 POINTS" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati timu yake inasewera mwapamwamba moti ikanatha kupambana mmasewero omwe yalepherana ndi FCB Nyasa Big Bullets koma mipata yomwe anayipeza aphonya.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe alepherana 0-0 pa bwalo la Nankhaka ndipo wati zolakwika zonse akonza kuti mmasewero awo ndi MAFCO adzapambane.
"Tiyamike Mulungu kuti takumana ndi anzathu a Nyasa Big Bullets, tithokozenso anyamata athu asewera bwino kwambiri mwina zangochitika koma bwenzi tikuti Blue Eagles yatenga 3 points koma tikonza molakwika kuti ndi MAFCO tidzapambane." Anatero Kananji.
Kutsatira zotsatirazi, Blue Eagles yasuntha mu ligi ya TNM pomwe tsopano yafika pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) ndi mapointsi 35 pa masewero 29 mu ligiyi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
"UKAYENDA MASEWERO AMAKHALA OVUTA" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Heston Munthali, wati timu yake yasewera bwino komabe akakhala kuti akasewera koyenda amadziwa kuti masewero amakhala ovuta kwambiri.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 ndi timu ya Blue Eagles pa bwalo la Nankhaka ndipo wati masewerowa anali ogundana kwambiri mpake sanasewere bwino.
"Tithokoze osewera athu poti tapeza point imeneyi, anali masewero ovuta kwambiri mchigawo choyamba sitimakhazikitsa mpira pansi koma mchigawo chachiwiri tinapeza mipata yomwe taphonya. Anali a masewero a physical kwambiri ndi zoti osewera athu amafunika kutetezedwa komabe ma Yellow card ambiri apita kwa ife iwo ayi." Anatero Munthali.
Timuyi yatsala ndi masewero atatu kuti imalize ligi ya chaka chino ndipo ili ndi mapointsi 56 pa masewero 27 omwe yasewera. Timuyi ikutsogola ndi mapointsi awiri pamwamba pa Mighty Mukuru Wanderers.
SAD NEWS
Ghanaian international Raphael Dwamena has died after collapsing on the pitch while playing for his Albanian side KF Egnatia this afternoon.
The former Real Zaragoza and Levante forward has died at the age of 28 and the Republic of Albania has cancelled all football matches in the wake of his death.
Video footage being shared online show the Ghanaian collapsing on the pitch while running and immediately the referee stopped the game and medics rushed to attend to him.
Efforts to resuscitate him failed.
Rest In Peace Raphael 🙏🏽
RED LIONS YATULUKA MU SUPA LIGI
Timu ya Red Lions ikubwereranso ku ligi yaying'ono yakummwera kwa dziko lino ya Thumbs Up Southern Region Football league pomwe yatuluka muligiyi loweruka angakhale kuti sinasewere masewero kamba koti MAFCO yatola pointi lero.
Lions inali ndi 29 points ndipo pamafunikira kuti adzagonjetse Moyale Barracks ndi zigoli zodutsa 13 komanso kuti MAFCO isatole pointi iliyonse koma maloto amenewo akanika.
MAFCO yatola pointi imodzi kuti ifike pa mapointsi 33 chimodzimodzi Ekwendeni Hammers komanso Civo United yomwe Red Lions singafikire kuti itsatire Extreme FC kotuluka. Awa ndi matimu ena omwe ali pa chiopsezo chotuluka.
8. Dedza Dynamos 28 -8 35 9. Blue Eagles 28 1 34 10. Mighty Tigers 27 -2 34 11. Civo United 28 0 33 12. MAFCO 28 -8 33 13. Ekwendeni Hammers 29 -12 33 14. Moyale Barracks 28 -7 31
Reported by Hastings Wadza Kasonga Jr
tiyen tilimbikile chikho titengeso
Hy hy hy gyz bullets fc mbambande
Im fine is to goal so have of to time
CASTEL CUP ROUND OF 16 DRAW
1. Soche Socials / FCB Nyasa Big Bullets vs Civil Service United 2. Silver Strikers vs Ekwendeni United 3. Red Lions vs Mighty Mukuru Wanderers 4. Chitipa United vs White Eagles 5. Bangwe All Stars vs MAFCO 6. Moyale Barracks vs Mighty Tigers 7. Dedza Dynamos vs Ekwendeni Hammers 8. Kamuzu Barracks vs Blue Eagles
CASTEL CHALLENGE CUP QUARTER FINAL DRAW
1. Silver Strikers | Ekwendeni United vs Kamuzu Barracks | Blue Eagles
2. FCB Nyasa Big Bullets / Soche Socials | Civo United vs Dedza Dynamos | Ekwendeni Hammers
3. Red Lions | Mighty Mukuru Wanderers vs Mighty Wakawaka Tigers | Moyale Barracks
4. Chitipa United | White Eagles vs Bangwe All Stars | MAFCO
Katswiri wa timu ya FCB Nyasa Big Bullets, Precious Phiri wasankhidwa kukhala wosewera wapamwamba kuposa onse mu mwezi wa October kutimuyi.
Iye wapamwamba mphotoyi kachiwiri motsogozana kutimuyi atapeza mavoti ochuluka kuposa Ephraim Kondowe and Rabson Chiyenda.
Iye anapambananso mu mwezi wa September pa mphoto yaku timuyi.
KB YASAMUTSA CHITIPA KU PLOT 4
Timu ya Kamuzu Barracks yalimbitsa mwayi wawo womaliza pa nambala yachinayi mu ligi ya TNM pomwe yachotsa timu ya Kamuzu Barracks pa malopa atagonjetsa Extreme FC 1-0 pa bwalo la Civo lachitatu.
Sheriff Maulana anamwetsa chigoli chopambanira pa mphindi 89 zamasewerowa kuti KB ipeze mapointsi atatu zomwe wachiwiri kwa mphunzitsi wawo, Ted Kalinda anakondwera kwambiri.
"Tithokoze Mulungu kamba koti tapambana, masewero anativuta mchigawo choyamba poti anyamata anali ndi phuma kuti akapambana afika pa nambala yachinayi nde timangotaya mipira koma titawayankhula anakonza mpaka tinapeza chigoli." Anatero Kalinda.
Iye wati timuyi ichilimika kuti imalizire pa nambala yachinayiyi pomwe tsopano ili ndi mapointsi 45 pa masewero 28 ndipo singakwanitse kutenga ligi kapena kufika pa nambala yachitatu.
"TAGONJA NDI TIMU YABWINO" - KAFOTEKA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Extreme FC, Elvis Kafoteka, wati chibwana ndi chimene chawapangitsa kuti asachite bwino mmasewero awo pomwe agonja 1-0 ndi timu ya Kamuzu Barracks pa bwalo la Civo lachitatu.
Iye amayankhula izi atatha masewerowa omwe anachinyitsa nthawi yothayitha ndipo iye wavomereza kugonjaku ponena kuti agonja ndi timu yabwino.
"Tagonja ndi timu yabwino kwambiri, yasewera bwino kwambiri koma ifeyo tikanatha kupambana koma taphonya mipata yathu kamba ka chibwana nde sitikanapambana." Anatero Kafoteka.
Timu ya Extreme inakhala yoyamba kutuluka mu ligi ya TNM pomwe pano ili ndi mapointsi 18 pamasewero 29 omwe yasewera ndipo mmasewero otsiriza, idzakumana ndi Chitipa United.
RED LIONS IKUFUNIKIRA ZIGOLI 13 KUTI ITSALE MU LIGI
Moyo wa timu ya Red Lions kuti isatuluke mu ligi ya TNM ya chaka chino ukunka nucheperabe pomwe tsopano ikufunikira zigoli 13 kuti idzapambane pomwe idzakumane ndi Moyale Barracks mmasewero omaliza.
Timuyi yalepherana 1-1 ndi FCB Nyasa Big Bullets pa bwalo la Balaka ndipo kupambana kwa Ekwendeni Hammers pa Civo United 3-2 kwaononga moyo wawo pomwe maso awo akuyang'ana pa MAFCO yomwe ili pa nambala 13 ndi 32 points.
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimuyi, Chifundo Masapula, yemwe nthawiyi samadziwa zotsatira za masewero ena, anati ngati moyo ulipobe, akalimbikira posewera ndi Moyale.
"Sitikudziwa kuti mmene anzathu asewera kuti zili bwanji komabe ngati agonja ndekuti ndi Moyale tidzapita ndi mphamvu zonse kuti tidzachite bwino." Anatero Masapula.
Lions ili ndi mapointsi 29 pa masewero 29 omwe yasewera mu ligiyi ndipo ikadali pa nambala 15 mu ligiyi.
"TIMADZIWA KUTI SAKHALA MASEWERO OPHWEKA" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati amadziwa kuti masewero awo ndi timu ya Red Lions akhala ovuta kamba koti nawo amamenyera nkhondo yoti atsale mu ligi.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe analepherana 1-1 ndi timu ya Red Lions pa bwalo la Balaka ndipo anati point yomwe anatengayo ndi yamphamvu poti iwathandiza kumbali ina.
"Timadziwa kuti akhala masewero ovuta ndipo anzathuwa abwera movuta poti akufuna atsale mu ligi koma anyamata analimbikira ndipo asewera bwino, tinapeza chigoli koma iwo anabwenza, mmasewero omwe atsalawa tiyesetsa kuti tikachite bwino." Anatero Munthali.
Zipambano ziwiri pa masewero anayi omwe timuyi yatsala nawo ziwathandize kutenga ukatswiri wa chaka chino pomwe ali ndi mapointsi 55 pa masewero 26 omwe yasewera.
MATIMU AKUMPOTO AKUKANIRANA KUTULUKA
Nkhondo yozimenyera nkhondo yotsala mu ligi ya TNM yavuta kwambiri pomwe timu ya Ekwendeni Hammers yakankhira ku chigwa cha matimu otuluka timu ya Moyale Barracks kutsatira kugonjetsa Civo 3-2 pa bwalo la Rumphi lachitatu.
Sammy Phiri, Wongani Lungu ndi Blessings Singini anagoletsa zigoli za Hammers pomwe Binwell Katinji ndi John Dambuleni anamwetsa za Civo zomwe zinakondweretsa mphunzitsi wa Hammers, Elias Chirambo.
"Tithokoze Mulungu kuti anali mbali yathu komanso tiyamike anyamata kuti asewera bwino mpaka tapambana. Tinali koti titha kutuluka koma tachokako, masewero atsalawa tiyesetsa kuti tidzapambanenso." Anatero Chirambo.
Asanayambe masewerowa, Hammers inali pa nambala 14 koma kutsatira kupambanaku, iwo afika pa nambala 11 ndi mapointsi 33 pa masewero 29 mu ligiyi.
"SITIKUDANDAULA KUTI TAGONJA SIZIKUOPSA" - CHIDATI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civo United, Wilson Chidati, wati timu yake sikudandaula kuti agonja ndi Ekwendeni Hammers mu ligi ya TNM pomwe wati sizikuopsa kuti atha kutuluka.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 3-2 pa bwalo la Rumphi ndipo wati amadziwa kuti akhala ndi masewero ovuta nde ayang'anabe mmasewero awiri omwe atsala nawo.
"Tagonja inde komabe tiwayamikire anyamata kuti asewera bwino, timadziwa kuti akhala masewero ovuta potengera ndi manambala a matimu onsewa koma takwanitsa kugoletsa zigoli ziwiri koyenda, anyamata agwira ntchito." Anatero Chidati.
Timuyi ikadali pa nambala 10 mu ligi ya TNM ndi mapointsi okwana 33 mu ligiyi ndipo ikufunikira kupambana mmasewero awo omwe atsala nawo kuti alimbitse mwayi wotsalamu ligiyi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr.
PHODO, MFUNE NDI CHIYENDA SAPEZEKA NDI RED LIONS
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati osewera ake atatu, Maxwell Gasten Phodo, Antony Mfune komanso goloboyi Rabson Chiyenda sapezeka pa masewero omwe akumane ndi Red Lions kamba kovulala.
Iye wayankhula izi patsogolo pa masewerowa omwe achitike pa bwalo la Balaka lachitatu ndipo wati anyamata ake akonzekera kuti akachite bwino mmasewerowa.
"Anyamata akonzekera bwino kuti tikapambane, tikukumana nawo oti ali pa chiopsezo choti atha kutuluka komanso amatipatsa mavuto komabe tikuyenera kupita ndi mtima wonse kuti tikapambane." Anatero Munthali.
Timu ya Bullets ikungofunako mapointsi asanu ndi imodzi (6) kuti apambane ligi ya chaka chino pa masewero asanu omwe atsala nawo kuti amalize ligiyi.
"NDIWINA UTSOGOLERI WA FAM" - VINGULA
Mmodzi mwa anthu omwe aonetsa chidwi choimira pa mpando wa utsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi, Balawala Vingula, wati anthu asadere nkhawa poti apambana zisankhozi.
Iye amayankhula izi pa wayilesi ya Angaliba FM madzulo a lachiwiri ndipo wati pofika pa 14 November, dzina lake likhala litamveka kuti wasankhidwa kuti akayime nawo pa chisankhochi.
"Nomination atseka pa 15 November koma ikamadzati 14 mudzamva kuti dzina langa alipanga nominate ndipo pa zisankhozi ndikukawinanso ndi ine." Anatero Vingula.
Padakali pano, mtsogoleri wa bungweli, Walter Nyamilandu Manda komanso mtsogoleri wa Bungwe la Super League of Malawi, Fleetwood Haiya ndi omwe alandira kale ma nomination.
Lanjesi akangomwetsako pa Balaka basi golodeni buuti atenga Chaka chino
What deference fcb end mighty mukulu
Wamkaka