"SILVER NGATI TIMU YAIKULU IMAFUNIKIRA PA 1 KAPENA 2" M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wati kupambana mmasewero awo omwe akusewera ndi timu ya Chitipa United lachitatu ku Karonga ndi kufunikira poti iwo ngati timu yaikulu amafunikira kukhala pabwino.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewerowa pa bwalo la Karonga ndipo wati timu yake yakonzeka kwambiri.
"Takonzekera kwambiri pa masewero amenewa kutengera kuti tinataya mapointsi ndi Karonga koma osewera amadziwa kuti akamachita bwino amapeza ndalama nde kupambana ndi Chitipa kukhala kofunika kwambiri."
"Mukudziwa kuti Silver Strikers ndi timu yaikulu nde ngati timu yaikulu tikuyenera kumakhala pa nambala yoyamba kapena yachiwiri nde kupambana nkofunika." Anatero M'gangira.
Timu ya Silver Strikers ili pa nambala yachitatu ndi mapointsi okwana 47 pa masewero 26 omwe yasewera.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores