"TINALI NDI MIPATA YAMBIRI YOTI TIKANATHA KUPAMBANA" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Trevor Kajawa, wati ndi wokondwa kamba koti timu yake yapeza point imodzi pamwamba pa timu ya Silver Strikers ndipo wati ziwathandiza mmasomphenya awo omaliza pabwino.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 pa bwalo la Karonga ndipo anati anyamata ake anasewera bwino kuposa Silver Strikers.
"Anali masewero abwino kwambiri, kuimitsa timu ngati Silver Strikers ndekuti anyamata achita bwino kwambiri. Tinali ndi mipata yambiri yoti tikanatha kupeza zigoli, Silver inangopeza mpata umodzi mchigawo chachiwiri komabe point imodzi ndi yabwino." Anatero Kajawa.
Iye anati pa masewero atatu omwe atsala nawo ndi FCB Nyasa Big Bullets, Bangwe All Stars komanso Mighty Wakawaka Tigers, ayesetsa kuti achite bwino. Karonga ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi ndi mapointsi 37 pa masewero 27.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores