"KUPHA BULLETS KULIBE TANTHAUZO LILILONSE MU TNM" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civo United, Abbas Makawa, wati timu yake ikuyenera kuchilimika kuti ipeze chipambano pamwamba pa timu ya Dedza Dynamos pomwe wati iwo sali pabwino.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewero a matimu awiriwa pa bwalo la Civo ndipo iye wati kugonjetsa timu ya FCB Nyasa Big Bullets mu Airtel Top 8 kulibe phindu poti ndi zosiyana ndi ligi ya TNM komwe kuli moyo wawo.
"Zokonzekera zikuyenda bwino ndipo tikuyembekezera masewero ovuta kwambiri poti ife sitili pabwino pomwe Dedza ikufuna kuthera mu Top 8 nde anyamata tawauza kufunikira kopambana. Za Airtel sizikugwirizana ndi za TNM nde tikuyenera kupanga za masewerowa." Anatero Makawa.
Timu ya Civo ili pa nambala yachikhumi ndi chiwiri (12) pomwe ili ndi mapointsi okwana 30 ndipo ikusiyana mapointsi awiri ndi Moyale Barracks komanso Red Lions omwe ali ku chigwa cha matimu otuluka.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores