ZA KHUDA AKUTI:
Katswiriyu wathetseredwa mgwirizano kamba koti si womwetsa zigoli yemwe amamufuna pomwe akuti akutsalira kwambiri pa wosewera yemwe amamufuna.
Timu ya Tishreen SC ikufuna kuteteza chikho chimene inatenga chaka Chatha ndipo pano ali pa nambala yachisanu mu ligi ya chaka chino.
Khuda wasewera masewero anayi ndipo sanagoletse chigoli chilichonse ndipo dzulo atangosewera masewero omwe anagonja 2-0 pa kwawo, ochemerera anaonetsa kusakhutira ndi ntchito zake ndipotu patangodzutsa maola awiri, iyetu amuthetsera mgwirizano.
Akuti kusachita bwino kwa timuyi ndi Khuda komanso ndi wolemedwa kwambiri ndipo samadziwa poti azipezeka monga iye womwetsa zigoli.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores