"BWALO SILABWINO SITIKANAMENYA MPIRA WATHU" - M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wati timu yake inayesera kusintha kaseweredwe kamba koti bwalo la Karonga silabwino koma zinavutabe ndipo wati ndi zowawa kufanana mphamvu.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe analepherana 0-0 ndi Karonga United ku Karonga ndipo anati anali masewero omwe akanatha kupambana mosavuta koma aphonya kwambiri.
"Kusintha kumene tinasintha ndi chifukwa choti bwaloli silabwino, sitikanatha kupatsirana ndi kumenya mpira wathu mpake tinalowetsa osewera ataliatali komabe taphonya kwambiri ndi zotsatira zowawa kwambiri." Anatero M'gangira.
Timu ya Silver Strikers ili pa nambala yachitatu ndi mapointsi okwana 47 pamasewero 26 omwe asewera mu ligi ya TNM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores