"OSEWERA ATOPA KOMA SITINGACHITIRE MWINA" - M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wati timu yawonso ikhonza kukhala ndi madando oti osewera atopa koma poti palibe chomwe chingasinthe iwo amalizitsabe kusewera.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Ekwendeni Hammers pa bwalo la Bingu loweruka ndipo wati timu yake yakonzeka kwambiri.
Iye wati osewera onse apezeka pomwe omwe anali ovulala achira ndipo pa nkhani ya kutopa, iye wati adziwa mongowagwiritsa ntchito mwake.
"Ndi nkhani yoti atopadi koma poti kuno ndi ku Malawi, kudandaula palibe chomwe chingasinthe nde nkhani ndi kungodziwa kuwagwiritsa osewerawa kuti onse asamatope." Anatero M'gangira.
Timu ya Silver inapambana 3-1 mu chigawo choyamba pa bwalo la Mzuzu ndipo ikupita mmasewerowa ili pa nambala yachitatu ndi mapointsi 50 pamasewero 27 omwe yasewera.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores