"MMENE ZIKUYENDERA SIZIKUNDIKONDWERETSA" - NGINDE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, MacDonald Mtetemera, wati sakukondwa ndi mmene timu yake ikupatsidwira masewero osiyanasiyana zomwe zikuchititsa kuti osewera azitopa.
Nginde amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Silver Strikers pa bwalo la Karonga ndipo wati timu yake sikupatsidwa ulemu popereka masewero.
"Kunena zoona masewero tikusewera pafupifupi ndipo anyamata tsopano akutopa nanga taonani chichokereni kunyumba popita ku Blantyre tinadutsa ku Rumphi mpaka pano sitinafike nde mmene zilili sizikundikondweretsa ndipo sakutipatsa ulemu ndi mmene akuchitira." Anatero Mtetemera.
Kumbali ya masewero, iye wati chilichonse chikhonza kuchitika pa bwalo la zamasewero. Chitipa United ili pa nambala yachinayi ndi mapointsi 44 pa masewero 27.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores