OYIMBIRA NDI A BEACH SOCCER APEREKEZA HAIYA
Mabungwe awiri omwe amakhudzidwa nawo pa zisankho za bungwe la Football Association of Malawi a Oyimbira komanso a beach Soccer asankha dzina la mtsogoleri wa Super league of Malawi, Fleetwood Haiya, kuti akaime nawo ngati mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi.
Zadziwika ndi Zodiak kuti mabungwe awiriwa akufunitsitsa kuti a Haiya omwe angolowa pa mpando wa ku SULOM chaka chathachi akapikisane nawo pa mpandowu pa chisankho cha pa 16 December chaka chino.
Haiya atafunsidwa ngati ayime pa chisankhochi, sanakane kapena kuvomera koma anati ayankhapo ndipo ndi kusankhidwaku, iye akuyenera kuyimira.
Ngati iye apange chiganizo choti ayimire, mpando wake waku SULOM ndekuti awusiya ndipo utsogoleredwa ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa bungweli.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr (Source: Zodiak)
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores