Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
Cp United fayaaaaaaaa!!
I need fixture for fdh cup 2023
FDH Bank Cup fixture updated.
Mukuru mighty wanderers
I hope to see a clean sheet ...and 1 or so goals to come
Manoma
CHIMANGO KAYIRA WASIYA MPIRA
Katswiri wa Bangwe All Stars, Chimango Kayira walengeza za kusiya kwa masewero ampira wamiyendo atatumikira matimu osiyanasiyana kwa zaka 15 lachisanu.
Kayira anakamba izi pomwe amalengeza kuti wapeza ntchito yatsopano ku Mpira Mmudzi Mwathu Organization ngati Project Officer kumeneku.
Iye wathokoza matimu onse omwe wasewerako kamba komupatsa zoyenerera kuti akathe kuchita bwino mmasewero ake.
Iye wasewerako FCB Nyasa Big Bullets, Escom United mdziko muno komanso Costa Do Sol ndi AD Vilankulo kunja kwa dziko lino.
SAKA WAPITA KU TIGERS
Timu ya Karonga United yalengeza kuti katswiri wawo, Steve Saka, akupita kutimu ya Mighty Wakawaka Tigers pangongole kwa miyezi isanu.
Timuyi yalengeza nkhaniyi lachisanu ndipo iye tsopano akhonza kupezeka mmasewero omwe Tigers ikumane ndi Bangwe All Stars lachitatu likudzali.
Katswiriyu anachokera kutimu ya Dwangwa United kuti azipita ku Karonga.
MHANGO WACHOTSEDWA KU AMAZULU
Timu ya Amazulu yatulutsa ndandanda wa osewera omwe sakhala limodzi ndi timuyi mu ligi ya chaka cha 2023 mpaka 2024 ndipo dzina la Gabadinho Mhango lili poyanbilira.
Zamveka kwa kanthawi tsopano kuti Amazulu sikumufuna katswiriyu ndipo wakhudzidwa ndi mphekesera zoti atha kupita ku Kaizer Chiefs. Mayina onse omwe akuchoka ku Amazulu ndi awa:
1. Gabadinho Mhango 2. Rally Bwalya 3. Lehlohonolo Majoro 4. Keegan Buchanan 5. Dumisani Zuma 6. Jean Noel Amonome 7. Thendo Mukumela 8. Lankie Khoza 9. Thabo Qalinge 10. Sbongakonke Ndlovu 11. Kabelo Makola 12. Samkelo Mgwazela 13. Sphelele Zulu 14. Jody February (loaned from Sundowns) 15. Guily Manziba
WANDERERS YAMVANA NDI MADINGA
Katswiri wa Flames, Francisco Madinga, tsopano akuyembekeza kusaina mgwirizano wake ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers pomwe mbali zonse ziwiri tsopano zamvana pa zimene akufuna.
Madinga anabwera mdziko muno atathetsa mgwirizano wake ndi timu yaku Botswana ya Jwaneng Galaxy kamba kosowa mpata osewera ndipo anapita ku Amazulu kukayesa mwai komwe sizinatheke.
Iye anayamba zokonzekera ndi timuyi pomwe amakambirana Kaye kamba koti amafuna kusaina mgwirizano wa chaka chimodzi koma Wanderers imakana.
Nkhani yamveka tsopano kuti mbali zonse zamvana chimodzi ndipo Madinga awoneka ku Manoma mchigawo chachiwiri pomwe akhale akusaina mgwirizano wake.
NTHALA ALI KU SOUTH AFRICA
Mphunzitsi wamagoloboyi kutimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Simplex Nthala, ali mdziko la South Africa komwe akukaonjezera nzeru za maphunziro ku bungwe la COSAFA.
Nthala anapita mdzikoli sabata yatha ndipo akachitabe maphunzirowa pamodzi ndi anthu ena ammaiko akummwera kwa Africa.
Fdh cup
WANDERERS IKUFUNA AARON
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers ikuyembekezeka kupereka pempho la ndalama kutimu ya Civo United kuti itenge katswiri wawo wapakati, Lloyd Aaron, kuti apite kutimuyi.
Malipoti akuonetsa kuti timuyi sinafikire Civo koma ikukonza zotero kuti alimbitse timu yawo mchigawo chachiwiri.
Aaron wadziwika kwambiri ku mpikisano wa COSAFA pomwe anasewera mwapamwamba ndi timu ya Flames. Manoma ali pa nambala yachinayi mu ligi ya TNM pomwe yatolera mapointsi 28 pa masewero 15.
NOMA IKUFUNA K83 MILLION PA KUMWEMBE
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yati ikufuna ndalama yokwana K83 million pa mnyamata wawo, Christopher Kumwembe, kutimu yaku Zambia, Green Buffaloes yomwe ikufuna katswiriyu.
Mkulu watimuyi, Roosevelt Mpinganjira, watsimikiza zoti timuyi inalandira kalata kuchokera ku timu yaku Zambia imeneyi kuti akufuna katswiriyu atamuona ku mpikisano wa COSAFA Cup ku South Africa koma Manoma sali okonzekera kugulitsa osewerayu.
Koma malingana ndi malipoti a tsamba la Bola News, timu ya Wanderers inauza Buffaloes kuti ipereke ndalama yokwana $73 million yomwe ndi pafupifupi K83 million.
Kumwembe anagoletsa chigoli chimodzi ku COSAFA ndipo wamwetsa zigoli 7 mu masewero khumi omwe wasewera mu ligi ya chaka chino.
DEDZA IKUKANIZA NYONDO KUPITA KU SILVER
Timu ya Dedza Dynamos yati sikufuna kulora katswiri wawo womwetsa zigoli, Clement Nyondo, kuti apite kutimu ya Silver Strikers ngakhale kuti timuyi yalonjeza chithumba kwa osewerayu.
Malipoti akuonetsa kuti timuyi yalonjeza ndalama yokwana K450,000 kuti azilandira pamwezi ndiponso K5 million ngati angasaine mgwirizano ndi timuyi.
Koma zamveka kuti Dynamos sili yokonzeka kugulitsa katswiriyu pakatikati pa ligi ya chaka chino pomwe wagoletsa zigoli 11 pa zigoli 19 zomwe timuyi yamwetsa mu ligiyi.
Ndipo timu ya Silver Strikers ikufunitsitsabe Nyondo pomwe mphunzitsi watimuyi, Peter De Jongh, anadandaula kuti akuluakulu a timu yake anamunamiza kuti amugulira Hassan Kajoke ndipo tsopano akufuna katswiri womwetsa zigoli ngati Nyondo.
MALOYA AMADANDAULA NDI MMENE WANDERERS INAMUCHOTSERA
Katswiri wakale wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Aubrey Maloya, wayamba mwapamwamba mdziko la Mozambique pomwe sabata ziwiri zapitazo wagoletsa chigoli chake choyamba ndi timu ya Club Ferroviario de Quelimane mu ligi ya Moçambola.
Maloya anagoletsa chigolichi pomwe timu yake imakumana ndi timu ya Ferroviario de Nacala ndipo wati ndi wokondwa ndi mmene wayambira umoyo wake mdzikomo.
Iye wati amadandaula ndi mmene timu ya Mighty Mukuru Wanderers inamuchotsera poti anali asanaigwire ntchito imene iye ankafuna.
"Kubwera mwachangu ku Malawiko ndikovuta ndipo ku Wanderers ndinachosedwa ndisanayipangire zomwe ndimafuna, pokhapo ndimangodandaula koma aaah basi zimachitika kunoko akundisamalira kwambiri Zina zomwe kumeneko zimavuta kuno tikufewa." Maloya anafotokoza.
Iye anachotsedwa ndi Manoma pamodzi ndi osewera asanu ndi anayi ena ndipo wapita ku Mozambique mmwezi wa June.
BALIKINHO WASAINA ZAKA ZITATU KU NOMA
Katswiri wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Balikinho Mwakanyongo, wasaina mgwirizano wonjezera wa zaka zitatu ndi timuyi ngati njira yofuna kukhalitsira kutimuyi.
Mkulu watimuyi, Roosevelt Mpinganjira, watsimikiza za nkhaniyi pomwe wati timuyi ikufuna kukhalitsa ndi katswiriyu kuti agwire ntchito yomwe anaiyamba chaka chatha.
Mpinganjira watsimikizanso za kubwereranso kwa Francisco Madinga koma mgwirizano wake sanausaine kamba koti akuunika zinthu zina. Iye watinso Adeleke Kolawole sasaina mgwirizano wina poti ali ndi zaka ziwiri pa mgwirizano wake kale.
Mwakanyongo wabwera kutimuyi mwezi watha kutsatira kuchoka kutimuyi chaka chatha kulowera mdziko la Tanzania osatsanzika.
MUNTHALI WATHOKOZA BLUE EAGLES KOMANSO PETER MPONDA
Goloboyi wa timu ya Flames, Brighton Munthali, wathokoza timu ya Blue Eagles, komanso mphunzitsi wa mpira wamiyendo, Peter Mponda, kamba komuthandiza kupititsa patsogolo masewero ake a mpira.
Munthali walemba zimenezi pa tsamba lake la Facebook pomwe akusangalalira kuti akuyamba moyo watsopano wosewera kunja kwa dziko lino.
Iye wathokoza timu ya Blue Eagles kamba komutola pomwe luso lake limaoneka ngati likuguga koma timuyi inamuthandizira kuti azitolerenso. Iye wathokozanso osewera atimuyi kamba kogwira naye ntchito yomwe yamuthandiza kuti apitenso patsogolo.
Iye wathokozanso Peter Mponda koma Mr Philip Masiye, kamba komusula luso lake ku Sure stream Academy kuti adziwikenso ku dziko. Mponda ndiyemwe wasainanso katswiriyu ku timu ya Black Leopards mdziko la South Africa.
CHIMANGO KAYIRA AZILEMBA MU NYUZIPEPALA YA TIMES
Katswiri yemwe amasewera pakati mu timu ya Bangwe All Stars, Chimango Kayira, tsopano wapatsidwa mwayi kuti azilemba nkhani mu nyuzipepala ya Times yomwe izioneka lamulungu lokhalokha.
Katswiriyu watsimikiza za nkhaniyi lachinayi pomwe wati ndi okondwa kamba ka mwayiwu zomwe zimuthandize kuti akulitse luso lake lolemba ndikuziyika pamodzi ndi akatswiri odziwa kulemba.
Iye wati zolemba zake zoyamba zioneka pa 13 August 2023 lomwe ndi lamulungu ndipo wati tsatanetsatane yense amulembabe kuti anthu adziwe dzina la gawolo komanso zomwe zizikambidwa.
Anthu ochuluka anayamikira luso la kalembedwe ka katswiri wakale wa FCB Nyasa Big Bullets komanso Escom United ndipo anati kungakhale bwino atamalemba mu nyuzipepala.
"TIMAKONZA TSOPANO TIKOLOLE" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati timu yake tsopano ili bwino ndipo tsopano iyambe kukolola zomwe amafesa mchigawo choyamba.
Nyambose amayankhula izi atatha masewero omwe timu yake inalepherana 1-1 ndi FCB Nyasa Big Bullets pa bwalo la Kamuzu lachitatu. Iye anali osangalala ndi kaseweredwe katimuyi ndipo wati mchigawo chachiwiri, iwo agwira ntchito yaikulu.
"Timu yathu sinatuluke koma kungoti kubwera kwa osewera atsopano ku timuyi kunapangitsa kuti zina zizivuta koma tsopano takonza ndipo taona kusintha lero tagoletsa chigoli chabwinobwino pomwe ndi Blue Eagles timaphonya kwambiri apa tiyamba kukolola zomwe timalima." Anatero Nyambose.
Iye anatinso ndi okondwa poti timu yake sikuchinyitsa kwambiri pomwe wati ndi Chitipa yokha yomwe inagoletsa zigoli ziwiri pa iwo. Timuyi yamaliza pa nambala 14 ndi mapointsi 14 mu chigawo choyamba.
CHITIPA YATENGA CHINA
Timu ya Chitipa United yalengeza kuti yatenga katswiri wakale wa TN Stars, China Chirwa, kuti atumikire timuyi kwa miyezi isanu ndi umodzi (6).
Timuyi yalengeza izi lachinayi madzulo kudzera pa tsamba lawo la mchezo la Facebook pomwe ikufuna kulimbitsa kutsogolo kwawo.
Katswiriyu wapita ku timuyi pa ngongole kuchokera ku Silver Strikers ndipo akhala ku Chitipa kufikira mu mwezi wa December.
Chitipa United ili pa nambala yachitatu mu ligi ya TNM ndipo yagoletsa zigoli 18 mmasewero 15 amu ligiyi.
Mateu malensso
Airtel top 8 2023/2024 season draw
Help me with 2022 log table of the first round
MADINGA WABWERERA KU WANDERERS
Katswiri wa Flames, Francisco Madinga, wayamba zokonzekera ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers pomwe akuchita zokambirana kuti abwererenso ku timuyi.
Madinga anachoka mu 2022 pomwe anapita kutimuyi ya Dila Gori FC yaku Georgia komwe wasewerako chaka chimodzi ndipo anapitanso ku Jwaneng Galaxy yaku Botswana ndipo anapambanakonso chikho komabe wachoka kamba kosasewerasewera.
Iye anakayesanso mwayi ku timu ya Amazulu mwezi wathawu komabe wakanika kusaina mgwirizano ndi timuyi. Iye tsopano akuyembekezeka kuthandiza timuyi mu chigawo chachiwiri cha ligi ya TNM.
FLAMES SISEWERA NAWO CHAN
Bungwe loyendetsa mpira mdziko muno, Football Association of Malawi, lalengeza kuti timu ya dziko lino sisewera nawo masewero amu chikho cha CHAN cha chaka cha 2024.
Bungweli lanena izi ati kamba koti alibe ndalama zokwana zomwe zingawatheketse kuti atenge nawo mbali mu mpikisanowu.
Osewera omwe amasewera mmaligi a mdziko momwemo ndi omwe amaloledwa kusewera mu chikhochi.
BLUE EAGLES YAITANANSO KUWALI
Katswiri wa timu ya Blue Eagles, Schumacher Kuwali, waitanidwanso ndi timu yake kuti abwererenso pa bwalo la zamasewero pomwe timuyi isakuchita bwino mu ligi ya TNM.
Kuwali anaimitsidwa ndi timuyi mwezi watha kamba kosowa khalidwe kwa osewera anzake ndi aphunzitsi atimuyi koma pasanathe mwezi, timuyi yasintha ganizo lake.
Iye ayambe zokonzekera ndi timuyi pomwe ikukonzekera masewero awo otsatira ndi timu ya Silver Strikers.
Pakadali pano, Eagles yamaliza chigawo choyamba pa nambala 13 pomwe yatolera mapointsi 16 mmasewero 15.
PASUWA SATISFIED WITH BULLETS AFTER FIRST ROUND
FCB Nyasa Big Bullets head coach, Callisto Pasuwa, says he is satisfied with his team's performance in the first round despite a drop from 41 points last season to 30 points this season after first round.
The Zimbabwe said this after their 1-1 draw with Mighty Wakawaka Tigers saying the change is one of the things that happens in Football and the changing of players every year can be one of the leading factors.
"Very much satisfied about the performance, we did well remember we have been rejuvenating the team every year, finishing with these points we can't deny, it's one of the things that happen in the games." Pasuwa highlighted.
The tactician further said his team will be looking to sign at least two to three players to boost their squad ahead of the CAF Champions league plus to replace the injuries in the camp.
The team have finished top with 30 points where as Silver and Chitipa United have 29 points as the Nomads have 28.
"MAYBE IT'S A NEW RULE; NO TWO OR MORE PENALTIES" - PASUWA
FCB Nyasa Big Bullets head coach, Callisto Pasuwa, was left furious with how referee, Gift Chicco, performance during his team's match against Mighty Wakawaka Tigers after he denied three penalty appeals for the People's team in a 1-1 draw played at the Kamuzu Stadium.
The People's team missed their first half penalty which looked dubious after Hassan Kajoke was fouled in the box with a slight touch from Kelvin Banda then Innocent Nyasulu saved the effort from the team's number 9.
Meanwhile, a pressure in the second half made Bullets almost win two to three other penalties but Chicco looked not interested in all incidents, leaving Pasuwa furious after the game.
"I don't know the other side of where there's a new rule that a team mustn't get two penalties or even more than two, on that I need maybe to research." Said Pasuwa.
The People's team have finished the first round top with 30 points, a point ahead of Silver.
0:3
Gemu iti?
ZELIATI NKHOMA WACHIRA
Katswiri wa Kamuzu Barracks, Zeliati Nkhoma, akhale akubwereranso pa bwalo lazamasewero kumbali ya timuyi kutsatira kupeza bwino pomwe anavulala.
Katswiriyu anavulala kumayambiriro a ligi ya chaka chino ndipo sanapezeke kwa masabata odutsa khumi ndi atatu koma tsopano alibwino.
Nkhoma anatsimikiza za nkhaniyi kudzera pa tsamba lake la Facebook ndipo wati akuyembekezera kuti achita bwino kumbali yomwetsa zigoli mu ligiyi.
Katswiriyu anamwetsa zigoli zokwana khumi (10) chaka Chatha pomwe anathandizira KB kuthera pa nambala yachitatu mu ligiyi.
"ZOPITA KU KAIZER CHIEFS ZILI PATALI" - MAKAAB
Mkhalapakati wa katswiri wa dziko lino, Gabadinho Mhango, yemwe amatchedwa kuti Mike Makaab, watsutsa malipoti omwe amazungulira mdziko la South Africa kuti katswiriyu wasaina mgwirizano ndi timu ya Kaizer Chiefs.
Masiku atatu apitawa, masamba a mchezo ku South Africa, anadzadza ndi nkhani yoti Mhango wasaina ndi Chiefs komanso zina zinati akhale akuchita za Chipatala kutimuyi. Koma Makaab wati ulendo wake opita kutimuyi ukadali kutali ngakhale kuti Amazulu sikumufunadi.
"Sizoona zoti wasaina ndipo zoti akhonza kupita kumeneko zili patali kwambiri, kwa nthawi ino, Amazulu sikufuna zintchito za katswiriyu koma tikungounikira zina ndi zina poti ali pa mgwirizano ndi iwowo koma panopa tikukambirana ndi matimu osiyanasiyana." Anatero Makaab.
Kaizer Chiefs yakhala ikufuna katswiriyu pomwe zinamveka kuti Amazulu sikumufunanso ndipo tsopano malipoti aonetsa kuti Raja Casablanca yaku Morocco ikumuyang'ananso mwa chidwi.
Anold chimwenje
FDH cupleagie
Akatswiri odziwa kulosera bwino mpira sabata ino ndi Milako ndi Ernesto omwe agawana K15,000 atalosera molondola magemu osachepera 8 sabata yatha opa Owinna.
Pitani pa owinna.com nkulosera opanda mwaulere magemu ambiri kuti muchulutse mwayi wowina.
OFFICIAL
Sadio Mane has completed his move from Bayern Munich to Saudi Arabiaβs Al Nassr, joining Cristiano Ronaldo at the Riyadh club. The 31-year-old has signed a contract until 2027.
Moyale 1 silver 1
Mabodza
"TIKUIKHUMBA BULLETS MPAKE TAITSATIRA KU KAMUZU STADIUM" - ABAMBO
Mkulu watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Robin 'Abambo' Alufandika, wati timu yake ikuyikhumba timu ya FCB Nyasa Big Bullets kuti akaikhomere pakwawo pomwepo pomwe matimuwa akukumana lachitatu.
Abambo ati akuyembekezera kuti masewerowa kukhala ovuta kwambiri ponena kuti matimu onsewa ndi apamwamba kwambiri ndipo masewero akhalenso apamwamba.
"Mbambande mbambande, paja mukudziwa kale kuti ifeyo ndi timu mbambande ndipo Bullets ndi mbambandenso ndipo masewerowa akakhalanso mbambande. Ifeyo tachita kuwatsatira pa bwalo lawo chifukwa tikuwakhumba ndipo mubwere mawa mudzaone nokha." Watero Alufandika.
Matimuwa akumane mmasewero awo otsiriza a mu gawo loyamba ya ligi ya TNM Supa ligi ndipo chipambano cha Bullets chiwatengere pa mapointsi 32 pomwe Tigers idzafika pa mapointsi 16 ngati idzapambane.
SILVER YATI IDANA SAKUCHOKA
Timu ya Silver Strikers yatsutsa mphekesera zomwe zayenda pa tsamba la mchezo kuti katswiri wawo, Chimwemwe Idana, akuchoka kutimuyi pomwe yati anthu akumafalitsa nkhani zambiri zabodza.
Oyankhulira timuyi, Peter Masiye, wati akudabwa ndi zimene anthu akunenazi ndipo timuyi ikhale ndi Idana mpaka kumapeto kwa ligi ya chaka chino.
"Mgwirizano wa ife ndi Idana ukadalipo ndipo tangodabwa nazo nkhani zimenezi koma ndikufuna nditsimikizire onse otsatira ma Banker kuti Idana ndi wathu ndipo timaliza naye chaka chino." Anatero Masiye.
Idana anapita kutimuyi pangongole kuchokera ku timu ya Mbeya FC yaku Tanzania ndipo Silver inalengeza mu June kuti osewerayu akhalebe kutimuyi koma sanafotokoze mgwirizano weniweni pa katswiriyu.
Liverpool have confirmed Virgil van Dijk as their new club captain.
Trent Alexander-Arnold has been promoted to the role of vice-captain.
MSIKA WOGULA NDI KUGULITSA OSEWERA WATSEGULIDWA
Msika wogula ndi kugulitsa osewera mu ligi ya TNM mdziko muno watsegulidwa lachiwiri pomwe matimu akhale akuonjezera osewera mu matimu awo osiyanasiyana.
Bungwe la Super League of Malawi linalengeza za nkhaniyi sabata yapitayo ndipo linati msikawu ukhala kwa masabata awiri ndipo udzatsekedwa usiku wapa 14 August 2023.
DEAL DONE
Fabinho's move from Liverpool to join Saudi Arabian side Al-Ittihad in a Β£40million deal has been confirmed.
The Brazilian midfielder will have Nuno Espirito Santo, formerly of Wolves and Tottenham Hotspur, as his new manager and N'Golo Kante and Karim Benzema as team-mates after signing a three-year contract with the club.
TEMWA WATENGA MPHOTO YOMWETSA ZIGOLI ZAMBIRI YACHIWIRI CHAKA CHINO
Katswiri wa Scorchers, Temwa Chawinga, wapamwamba mphoto ya osewera yemwe wagoletsa zigoli zambiri ku China kachiwiri chaka chokha chino pomwe watenga mphotoyi mu chikho cha China Football Association Women's dzana.
Temwa wapambana mphotoyi pomwe anamwetsa zigoli 15 zomwe zinathandiziranso timu yake kutenga ukatswiri wa chikhochi atagonjetsa Shanghai 2-0 ndipo zigoli za Wuhan Jiangda anagoletsa ndi Temwa ndi Tabitha Chawinga.
Iye wapambana mphotoyi kachiwiri mu chaka chino pomwe anatenganso mphoto ngati yomweyi pomwe anapambananso chikho Chinese Women's National Cup mmwezi wa April.
Ndipo mkulu wake, Tabitha, anatenganso mphoto ngati yomweyi ku Italy komwe amasewera pa ngongole ku timu ya Inter Milan ya amayi koma mgwirizano wake umatha.
Barcelona
fcb mawa ikuwina 3 kwa 1
Hy brox
BANGWE WATENGA KAMWENDO
Timu ya Bangwe All Stars, yatenga mphunzitsi watimu ya Mighty Wanderers Youth, Joseph Kamwendo, kuti akakhale wogwirizira pomwe akuyang'anabe mphunzitsi okhazikika.
Timuyi yalengeza za nkhaniyi lachiwiri molingana ndi mmene ankalengezera akumutsitsa udindo Mavuto Lungu kupita ku timu yaying'ono yawo.
Kamwendo athandizidwa ndi Joseph Semu Ndipo Dave Pashane akhale mphunzitsi wama Goloboyi watsopano pomwe Steve Madeira akhalebe Technical Manager.
Kamwendo sangamutengeretu kukhala mphunzitsi poti ali ndi chiphaso chauphunzitsi cha CAF C koma bungwe la Super League of Malawi limafuna aphunzitsi ayambire kukhala ndi CAF B ndi CAF A.
NYONDO AKUCHITABE BWINO MU LIGI
Katswiri wa Dedza Dynamos, Clement Nyondo, akupitilirabe kuchita bwino mu ligi ya TNM ya chaka chino pomwe lamulungu wagoletsa chigoli chake chachikhumi ndi chimodzi (11) mu ligiyi.
Nyondo anagoletsa chigoli pa mphindi 82 kuti apulumutse Dynamos pomwe inafanana mphamvu ndi Ekwendeni Hammers 1-1 pa bwalo la Dedza.
Chigolichi chamutengera iye kutsogola ndi zigoli ziwiri tsopano pa mwamba pa wachiwiri wake, Lanjesi Nkhoma, wa FCB Nyasa Big Bullets yemwe ali ndi zigoli zisanu ndi zinayi (9).
Kuchita bwino kwa katswiriyu kwachititsa kuti matimu a Silver Strikers komanso FCB Nyasa Big Bullets adyerere maso pa katswiriyu.
Ndidolo mwanayu
TABITHA WAPAMBANA KALE CHIKHO KU CHINA
Katswiri wa timu ya Scorchers, Tabitha Chawinga, wapambana chikho cha China Women's Football Association Cup pomwe wabwereranso mdziko la China.
Tabitha wabwerera mdzikomo kutimu ya Wuhan Jiangda kutsatira kutha kwa mgwirizano wake wa chaka chimodzi wapangongole kutimu ya Inter Milan ya ku Italy.
Iye anapambana mphoto ya osewera omwetsa zigoli zambiri mu ligi ya Serie A pomwe anamwetsa zigoli 23 koma Wuhan inati mgwirizanowu ukadzatha iye adzapitanso kutimuyi.
NYAMBOSE AKANALI NDI TIGERS
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, akadali ndi timuyi ngakhale kuti timuyi inalengeza kuti yamuchotsa ntchito kamba kosachita bwino.
Mphunzitsiyu anatsogolera timuyi mmasewero omwe analepherana 0-0 ndi timu ya Blue Eagles loweruka ndipo anabwerera ku zokonzekera patangotha tsiku limodzi chimuchotsereni.
Iye akuyembekeza kutsogolera timuyi mmasewero awo omaliza a ligi pomwe akumane ndi FCB Nyasa Big Bullets lachitatu.
STAND UP FOR CHAMPIONS!!!!
Mauricio Pochettino, guided Chelsea to his first ever title with the team in just 30 days after crowned the Champions of Premier League summer series on Sunday.
The Blues were given the trophy after defeating Fulham 2-0 in USA with goals from Thiago Silva on 22nd minute and Christopher Nkunku on 40th minute sealing the victory.
The team starts their league campaign next week as they play Liverpool in their opening match.
MBULU AMONGST TOP SCORERS IN MOZAMBIQUE
Malawi National Football team forward, Richard Mbulu, is amongst the Mozambican Moçambola league after netting 5 goals for Costa do Sol this season.
Mbulu has been one of the most reliable players for his club after being signed this year together with other three Malawians, Yamikani Chester, Lloyd Njaliwa and Chikoti Chirwa.
Meanwhile, the star is in a huge group of players who are coming second in goals after the top scorer, Dayo of UD Songo, is having 9 goals, four goals ahead of his closest competitors like Mbulu. This is the full list so far:
9 GOALS β’Dayo - UD Songo
5 GOALS β’Richard Mbulu - Costa do Sol β’Isac de Carvalho - Costa do Sol β’Raymond - Ferroviario de Beira β’Telinho - Ferroviario de Nampula β’Jesus - A. Black Bulls
4 GOALS β’Victor A. Black Bulls β’Melque - A. Black Bulls β’Maxwell - Ferroviario de Maputo β’Odilo - Ferroviario de Quelimane
H