MALOYA AMADANDAULA NDI MMENE WANDERERS INAMUCHOTSERA
Katswiri wakale wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Aubrey Maloya, wayamba mwapamwamba mdziko la Mozambique pomwe sabata ziwiri zapitazo wagoletsa chigoli chake choyamba ndi timu ya Club Ferroviario de Quelimane mu ligi ya Moçambola.
Maloya anagoletsa chigolichi pomwe timu yake imakumana ndi timu ya Ferroviario de Nacala ndipo wati ndi wokondwa ndi mmene wayambira umoyo wake mdzikomo.
Iye wati amadandaula ndi mmene timu ya Mighty Mukuru Wanderers inamuchotsera poti anali asanaigwire ntchito imene iye ankafuna.
"Kubwera mwachangu ku Malawiko ndikovuta ndipo ku Wanderers ndinachosedwa ndisanayipangire zomwe ndimafuna, pokhapo ndimangodandaula koma aaah basi zimachitika kunoko akundisamalira kwambiri Zina zomwe kumeneko zimavuta kuno tikufewa." Maloya anafotokoza.
Iye anachotsedwa ndi Manoma pamodzi ndi osewera asanu ndi anayi ena ndipo wapita ku Mozambique mmwezi wa June.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores