BALIKINHO WASAINA ZAKA ZITATU KU NOMA
Katswiri wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Balikinho Mwakanyongo, wasaina mgwirizano wonjezera wa zaka zitatu ndi timuyi ngati njira yofuna kukhalitsira kutimuyi.
Mkulu watimuyi, Roosevelt Mpinganjira, watsimikiza za nkhaniyi pomwe wati timuyi ikufuna kukhalitsa ndi katswiriyu kuti agwire ntchito yomwe anaiyamba chaka chatha.
Mpinganjira watsimikizanso za kubwereranso kwa Francisco Madinga koma mgwirizano wake sanausaine kamba koti akuunika zinthu zina. Iye watinso Adeleke Kolawole sasaina mgwirizano wina poti ali ndi zaka ziwiri pa mgwirizano wake kale.
Mwakanyongo wabwera kutimuyi mwezi watha kutsatira kuchoka kutimuyi chaka chatha kulowera mdziko la Tanzania osatsanzika.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores