TEMWA WATENGA MPHOTO YOMWETSA ZIGOLI ZAMBIRI YACHIWIRI CHAKA CHINO
Katswiri wa Scorchers, Temwa Chawinga, wapamwamba mphoto ya osewera yemwe wagoletsa zigoli zambiri ku China kachiwiri chaka chokha chino pomwe watenga mphotoyi mu chikho cha China Football Association Women's dzana.
Temwa wapambana mphotoyi pomwe anamwetsa zigoli 15 zomwe zinathandiziranso timu yake kutenga ukatswiri wa chikhochi atagonjetsa Shanghai 2-0 ndipo zigoli za Wuhan Jiangda anagoletsa ndi Temwa ndi Tabitha Chawinga.
Iye wapambana mphotoyi kachiwiri mu chaka chino pomwe anatenganso mphoto ngati yomweyi pomwe anapambananso chikho Chinese Women's National Cup mmwezi wa April.
Ndipo mkulu wake, Tabitha, anatenganso mphoto ngati yomweyi ku Italy komwe amasewera pa ngongole ku timu ya Inter Milan ya amayi koma mgwirizano wake umatha.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores