"TIKUIKHUMBA BULLETS MPAKE TAITSATIRA KU KAMUZU STADIUM" - ABAMBO
Mkulu watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Robin 'Abambo' Alufandika, wati timu yake ikuyikhumba timu ya FCB Nyasa Big Bullets kuti akaikhomere pakwawo pomwepo pomwe matimuwa akukumana lachitatu.
Abambo ati akuyembekezera kuti masewerowa kukhala ovuta kwambiri ponena kuti matimu onsewa ndi apamwamba kwambiri ndipo masewero akhalenso apamwamba.
"Mbambande mbambande, paja mukudziwa kale kuti ifeyo ndi timu mbambande ndipo Bullets ndi mbambandenso ndipo masewerowa akakhalanso mbambande. Ifeyo tachita kuwatsatira pa bwalo lawo chifukwa tikuwakhumba ndipo mubwere mawa mudzaone nokha." Watero Alufandika.
Matimuwa akumane mmasewero awo otsiriza a mu gawo loyamba ya ligi ya TNM Supa ligi ndipo chipambano cha Bullets chiwatengere pa mapointsi 32 pomwe Tigers idzafika pa mapointsi 16 ngati idzapambane.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores