CHIMANGO KAYIRA AZILEMBA MU NYUZIPEPALA YA TIMES
Katswiri yemwe amasewera pakati mu timu ya Bangwe All Stars, Chimango Kayira, tsopano wapatsidwa mwayi kuti azilemba nkhani mu nyuzipepala ya Times yomwe izioneka lamulungu lokhalokha.
Katswiriyu watsimikiza za nkhaniyi lachinayi pomwe wati ndi okondwa kamba ka mwayiwu zomwe zimuthandize kuti akulitse luso lake lolemba ndikuziyika pamodzi ndi akatswiri odziwa kulemba.
Iye wati zolemba zake zoyamba zioneka pa 13 August 2023 lomwe ndi lamulungu ndipo wati tsatanetsatane yense amulembabe kuti anthu adziwe dzina la gawolo komanso zomwe zizikambidwa.
Anthu ochuluka anayamikira luso la kalembedwe ka katswiri wakale wa FCB Nyasa Big Bullets komanso Escom United ndipo anati kungakhale bwino atamalemba mu nyuzipepala.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores