MUNTHALI WATHOKOZA BLUE EAGLES KOMANSO PETER MPONDA
Goloboyi wa timu ya Flames, Brighton Munthali, wathokoza timu ya Blue Eagles, komanso mphunzitsi wa mpira wamiyendo, Peter Mponda, kamba komuthandiza kupititsa patsogolo masewero ake a mpira.
Munthali walemba zimenezi pa tsamba lake la Facebook pomwe akusangalalira kuti akuyamba moyo watsopano wosewera kunja kwa dziko lino.
Iye wathokoza timu ya Blue Eagles kamba komutola pomwe luso lake limaoneka ngati likuguga koma timuyi inamuthandizira kuti azitolerenso. Iye wathokozanso osewera atimuyi kamba kogwira naye ntchito yomwe yamuthandiza kuti apitenso patsogolo.
Iye wathokozanso Peter Mponda koma Mr Philip Masiye, kamba komusula luso lake ku Sure stream Academy kuti adziwikenso ku dziko. Mponda ndiyemwe wasainanso katswiriyu ku timu ya Black Leopards mdziko la South Africa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores