Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
ASCENT ACADEMY ARE CHAMPIONS IN EUROPE!!!!!!!
Lilongwe based Sports Academy, Ascent Soccer, are the Champions of Rey Cup in Iceland after beating Prottur 1-0 in the final played on Sunday.
The team have finished the competition without a defeat and conceding a goal after making their brilliant performance in their first major tournament in Europe and star, Mwisho Mhango scored the lone goal.
Ascent became the second African Academy to take part in the competition and are the first from Africa to win the Cup.
Reported by Hastings Wadza Kasonga Jr
Tnm yafikapo eish
Rasmus HΓΈjlund β Manchester United!π¨
Man United have reached full agreement with Atalanta on the signing of Rasmus HΓΈjlund for a fee of around β¬70m (including add-ons). π©π°
The Striker will put pen-to-paper on a five-year contract.
[Fabrizio Romano]
Germany
netball
"KULIBE KUPUMA POPITA CHIGAWO CHACHIWIRI" - SULOM
Bungwe la Super League of Malawi (SULOM) lati kulibe kupumira chikatha chigawo choyamba ndipo masewero apitirabe mpaka chigawo chachiwiri cha ligi ya TNM.
Mlembi wamkulu wa bungweli, Williams Banda, watsimikiza za nkhaniyi pomwe wati kuchuluka kwa zikho zimene zikuseweredwa ndi chifukwa chimene chachititsa kuti matimu asapumire.
Izi ndi zosemphana ndi mmene zimachitikira mu ligi ya zaka za mmbuyo monsemu pomwe matimu amapuma kwa masabata awiri. Matimu enanso makamaka omwe anatumiza osewera ku Flames ku Mpikisanowu wa COSAFA, anadandaula kuti osewera awo sanapume ndipo kupumaku kukanawachitiranso ubwino.
Chigawo choyamba cha ligi ya chaka chino chifika kumapeto sabata ya mawa lachitatu pomwe matimu ena atamalize masewero kumapeto a sabata ino.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
DAVIE WAYAKA MOTO
Katswiri wa timu ya Silver Strikers, Stain Davie, akutsogola pa osewera omwe apezetsa timu yawo zigoli zambiri chaka chino pomwe akukhudzidwa mu zigoli 13 pa zigoli zomwe timu yake yamwetsa chaka chino.
Davie ali ndi zigoli zisanu ndi ziwiri (7) ndipo wathandizira zigoli zisanu ndi chimodzi (6) pa zigoli makumi awiri ndi chimodzi (21) zomwe timu ya Silver yamwetsa mu ligiyi.
Ndipo yemwe amasewera naye mu timuyi, Chimwemwe Idana, ali ndi zigoli zisanu komanso kuthandiza zigoli 7 kuti akhudzidwe mu zigoli 12 chimodzimodzi Lanjesi Nkhoma wa FCB Nyasa Big Bullets yemwe ali ndi zigoli 8 ndipo wathandizira zinayi (4).
BISA BISA BISA BISA BISA!! UDZAULULE ZIKADZAYENDA!!
Katswiri wakale wa Flames, Khuda Muyaba, waziona pomwe wakanidwa ndi mphunzitsi watimuyi, Peter De Jongh, kuti akatumikire timuyi.
Izi zikudza pomwe katswiriyu anakanika kusainirana mgwirizano ndi timu ya Cape Town Spurs yomwe imafuna kumutenga ndipo iye amayankhula ka mwano pomwe amakambirana naye.
"Ena akuona ngati ndisewera ku Malawi, dikirani ndilengeza pompano." Khuda Anatero.
Koma katswiriyu sanapatsidwe mgwirizano ndipo atabwerera kumudzi amafuna kubwerera ku Silver Strikers koma zamveka kuti De Jongh wayankha kuti aganize Kaye koma panopa ayi.
Khuda anapita ku South Africa mu 2021 pomwe anasaina mgwirizano ndi Polokwane City koma ubale wawo wathera pakhoti chaka chino.
OFFICIAL: Al Ahli have signed Riyad Mahrez from Manchester City for Β£30m on a 4-year contract.
π¨Official: Arsenal have unveiled an Arsene Wenger statue outside The Emirates.
Arsène Wenger will be guest of honour for the Emirates Cup match against AS Monaco on Wednesday, August 2, and will also be taking time to visit his statue in the forthcoming days.
Kodzeka
Brainz Mw
silver will take the cup
ASCENT ACADEMY YAPAMBANA 8-0 KU ICELAND
Timu ya Ascent Academy yomwe ili mdziko la Iceland, yayamba masewero a chikho cha Rey Cup mwapamwamba pomwe yagonjetsa Reykjavik yaku Iceland 8-0 lachinayi.
Katswiri wa timuyi, Mwiso Mhango, anagoletsa zigoli zitatu yekha pomwe Lameck Mithi, James Chibala, Yusuf Nathunga, Hermas Masinja komanso Blessings Lungu anamwetsa chigoli chimodzi aliyense kuti apambane masewerowa.
Wamkulu wa watimuyi, Thom Nkolongo, anali wosangalala ndi mmene osewera achisodzerawa anachitira mmasewero awo malingana ndi kupeza kwa Owinna.
"Maseweredwe mu masewero oyamba anali bwino kwambiri ndipo zinali zosangalatsa kuona osewera asewera mwapamwamba motere. Anyamata amasewera ndi mpira kuusunga ndi kupanga nawo chilichonse, asewera bwino ndithu." Anatero Nkolongo.
Mdzikomo, timuyi yasewerakonso masewero apaubale pomwe inapha UMFA 5-0 chipitireni kumeneko. Iyo ikumana ndi matimu enanso aku England ndi Germany mu mpikisanowu.
Sabata ino, Judth wawina K10,000 pomwe wotsatira wake, Xavier wawina K5,000 atalosera bwino magemu osachepera 7 pa Owinna.com!
Congratulations π
ππ Judth Lino & Xavier Kabango π₯π₯
Exitrm vs sliver
DONE DEAL
Nottingham Forest have signed Sweden forward Anthony Elanga from Manchester United on a five-year deal.
The 21-year-old moves on from Old Trafford, with Forest believed to have paid United a fee of Β£15m.
Mwakodzeka
Wilfried Zaha has completed his move to Galatasaray, signing a three-year deal with the Turkish club.
Who many game in super league
BALIKINHO WASEWERA MASEWERO KU WANDERERS
Katswiri yemwe anathawa ku timu ya Mighty Mukuru Wanderers chaka Chatha, Balikinho Mwakanyongo, wasewera masewero ake oyamba mu chaka chino ndi timuyi pomwe anachokera panja mmasewero omwe timuyi yagonjetsa Blue Eagles 1-0 lamulungu.
Balikinho analowa pomwe chigawo chachiwiri chimayamba ndipo anasinthana ndi Francis Mkonda. Iye anasewera ngati wapakati wopita kutsogolo osati motchinga ngati mmene amadziwikira.
Iye Γ nasintha zinthu pakati pa timuyi pomwe kulowa kwake, Wanderers inapeza chigoli cha masewerowa. Patatha mphindi 56, iye analandira kalata yachikasu kamba kosamufikira bwino Gilbert Chirwa.
Masewero otsatira omwe atha kusewera ndi pakati pa timuyi ndi MAFCO pa bwalo la Chitowe mu ligi ya TNM.
KUMWEMBE WAVULALA POMWE OSEWERA A FLAMES AKUVUTIKA
Katswiri wa Mighty Mukuru Wanderers, Christopher Kumwembe, anakanika kusewera masewero atimu yake ndi Blue Eagles pomwe anavulala akupanga zoziongola masewerowa asanayambe.
Kumwembe anayikidwa kuti ayambe panja koma anachotsedwa pa ndandanda wa osewera kamba koti anavulala. Mulingo wa kuvulala kwake sunalengezedwe ndi timuyi.
Anthu ambiri adabwa ndi mmene osewera omwe anali ndi Flames ku COSAFA akuvulalira pomwe Robert Saizi anangosewera mphindi 24 pamasewero omwe Bangwe All Stars inalephera 1-1 ndi Ekwendeni Hammers.
Osewera ena omwe anali ndi Flames koma sakupezeka kamba kuvulala ndi Chimwemwe Idana ndi Patrick Macheso onse a Silver Strikers.
Pajatu anthu ananena kuti ma players akanapuma kaye
OFFICIAL
Borussia Dortmund have signed Marcel Sabitzer from Bayern for a fee around β¬19m.
Marcel Sabitzer has signed a four-year contract until 2027.
2023 FIFA Women's World Cup
African Teams First Round Results
Nigeria π³π¬ 0-0 π¨π¦ Canada
Japan π―π΅ 5-0 πΏπ² Zambia
South Africa πΏπ¦ 1-2 πΈπͺ Sweden
Germany π©πͺ 6-0 π²π¦ Morocco
4 games = 3 defeatsβ 1 drawπ€ β½1 goal scoredβ 13 conceded β
NEXT FIXTURES
Spain πͺπΈ vs πΏπ² Zambia ( On Wednesday)
Australia π¦πΊ vs π³π¬ Nigeria ( On Thursday)
Argentina π¦π· vs πΏπ¦ South Africa ( On Friday)
South Korea π°π· vs π²π¦ Morocco ( On Sunday)
#FIFAWWC #Morocco #Nigeria #Zambia #SouthAfrica
HARRISON NOT HAPPY DESPITE A WIN
Mighty Mukuru Wanderers head coach, Mark Harrison, says he was not happy with his team's performance against Blue Eagles despite his team claiming a 1-0 win at the Kamuzu Stadium.
Harrison said this in a post match interview that he was only happy with the win as they have closed the gap on other teams but the performance of the team displeased him.
"I'm happy with the three points to close the gap I'm not happy with the performance, you know the performance was more worrying, see how we performed in the past two games and today we come with this, I'm only happy with the result but not performance." Said Harrison.
The win has taken the Nomads up to fourth with 25 points from 13 games, a points behind FCB Nyasa Big Bullets which tops the log table and level on points with Silver Strikers who have a game in hand.
"OSEWERA ASAMASANKHE MALO" - WISDOM
Katswiri wa Mighty Mukuru Wanderers, Wisdom Mpinganjira, wati iye anangochikhazikitsa kuti asewere pa malo omwe mphunzitsi watimuyi angafune kuti amuseweretse pomwe wasewera mmalo odutsa asanu mu ligi ya chaka chino.
Mpinganjira amayankhula izi atatha masewero a timuyi ndi Blue Eagles omwe anapambana 1-0 ndipo anasankhidwa kuti wasewera bwino kuposa ena. Iye anati akumalimbikira komanso kupanga zomwe mphunzitsi akufuna ndi pomwe akufuna kusewera.
"Ndinangochikhazikitsa kuti ndimenye pomwe coach akufuna, osewera samasankha malo nde ineyo ndimagwira ntchito basi."
Katswiriyu wasewerapo ngati wotchinga kumbuyo wa kumanja, kumanzere, osewera mmbali yakumanja ndi kumanzere komanso osewera kutsogolo cha mmbali mu masewero 13 omwe wasewera chaka chino.
"TIKAWAPHUNZITSE OSEWERA KUMWETSA ZIGOLI BASI" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wati akuyenera kukawaphunzitsa osewera ake akutsogolo kuti azimwetsa zigoli pomwe wati timu yake ikutaya mipata yochuluka.
Kananji amayankhula izi atatha masewero awo ndi Mighty Mukuru Wanderers omwe anagonja 1-0 pa bwalo la Kamuzu ndipo anayamikira osewera ake kuti anasewera bwino koma wati mipata yochuluka ikungotayika.
"Tikuyenera kuti tibwerere kuti tikakonze ndi kuwaphunzira osewera athu akutsogolo kuti azimwetsa zigoli, kusewera nde tikuchita bwino koma mipata nde tikuyitaya yambiri, tikudutsa mu nyengo yowawa kuti ziyamba kuyenda." Kananji anatero.
Timu ya Blue Eagles yagonja masewero asanu ndi imodzi otsogozana mu zikho zonse pomwenso yatuluka mu chikho cha FDH sabata yatha. Timuyi ili pa nambala 12 ndi mapointsi 15 pa masewero 14 ndipo amaliza chigawo choyamba pokumana ndi Mighty Wakawaka Tigers.
KAFOTEKA WATI SIKUNATHE KWA EXTREME
Mphunzitsi watimu ya Extreme FC, Elvis Kafoteka, wati timu ya Extreme FC sinatuluke mu ligi ndipo izikokera mmasewero omwe atsalawa kuti achoke ku chigwa cha matimu otuluka.
Kafoteka wayankhula izi timu yake itagonja ndi Dedza Dynamos ndi chigoli chakumapeto cha Charles Chipala pa bwalo la Civo pomwe wati akusowa chokamba poti samayenera kugonja. Iye wati timu yake ikufunika anyamata ena wowonjezera ndipo wati akadali ndi mwayi wokhazikika mu ligi.
"Mwayi ndi wambiri, apapa tatsala ndi masewero awiri mu chigawo choyamba ndipo tili ndi chigawo chachiwiri pomwe tikokere ma pointsi. Sindikudera nkhawa, anyamata akusewera bwino koma akungosowa kuikapo mtima omwe utipangitse kuti tizichita bwino." Iye anatero.
Chiyambireni ligi ya chaka chino, Extreme yapambana masewero amodzi ndi Wanderers ndipo yakwanitsa kupeza mapointsi 6 pa masewero 13 omwe yasewera mu ligiyi.