Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
Akutha azungu wose pasuwa mutinchani anthun
Wawa maule
Link ndi imeneyi? Tilosere zigoli mwina nkudyako bwino pa Christmas ๐ฒ๐๐
Liverpool vs Arsenal
https://owinna.com/uk/epl/2024
CHAWANANGWA RETURNS ON THE PITCH
Flames forward, Chawanangwa Kaonga, will play his first match since September 2nd after being included in ZANACO's travelling Squad to face Nkana FC at Sunset on Saturday in the Zambian Super League.
The speedy forward got injured when Flames played Guinea in a 2-2 draw at the Bingu National Stadium and has missed 13 games for the club this season.
His coming has been considered as a major boost for the Bankers as he is the talisman for the side. The former Silver Strikers forward has two goals in three games already this season.
Links
WANDERERS IKUKAMBIRANA NDI CHESTER
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yatsegula zokambirana ndi katswiri wawo wakale, Yamikani Chester, kuti abwererenso kutimuyi mgwirizano wake ukatha ku timu ya Coastal do Sol yaku Mozambique.
Chester anachoka ku Wanderers kumayambiliro a chaka chino atakanika kumvana ndi timuyi ndipo anasaina mgwirizano wa chaka chimodzi ku Mozambique komwe amachita bwinonso kwambiri.
Koma zamveka kuti katswiriyu sakufunanso kubwereranso ku dzikoli ndipo Manoma akufuna atatemganso ma busy.
Timuyi ikukambirananso ndi wosewera wa Civo, Lloyd Aaron, yemwe malipoti akuonetsa kuti mmodzi mwa aphunzitsi ku Flames anamuuza kuti asapite ku Wanderers poti samasamala osewera bwino komanso Clement Nyondo wa Dedza Dynamos yemwe akuopa kuti atha kumakangokhala panja Ku Nomaku.
Apite bass Mr bus
fifa world club cup
CHAWINGA RANKED AHEAD OF JAMES AND KERR IN GOAL50
Scorchers captain, Tabitha Chawinga, has been ranked fourth in the GOAL50 Top 10 Best Women's Players of 2023 ahead of Chelsea's and England's forward, Laureen James.
The list is released by one of the media outlets, GOAL.COM, and has recommended Chawinga after having an impressive performance in Italy with Inter Milan where she won the golden boot and player of the tournament award.
Meanwhile, Zambia's Rachael Kundakwanji came first while Asisat Oshoala of Barcelona women and Nigeria was second with Linda Caicedo of Real Madrid coming third.
James came out fifth behind Chawinga whereas Ballon d'Or second placed star, Sam Kerr was placed 9th on the list.
๐ฟ๐ฒ ๐๐๐๐ก๐๐๐ฅ ๐๐ฎ๐ง๐๐๐ง๐๐ง๐ฃ๐ข ๐ณ๐ฌ Asisat Oshoala ๐จ๐ด Linda Caicedo ๐ฒ๐ผ Tabitha Chawinga ๐ด๓ ง๓ ข๓ ฅ๓ ฎ๓ ง๓ ฟ Lauren James ๐ฏ๐ฒ Bunny Shaw ๐ช๐ธ Salma Paralluelo ๐ซ๐ท Kadidiatou Diani ๐ฆ๐บ Sam Kerr ๐ซ๐ท Grace Geyoro
MARK HARRISON ALI PA MPENI
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers ikulingalira zochotsa mphunzitsi wawo, Mark Harrison, kuti abwerere pa udindo wake ngati technical director kamba kokanika kutengetsa chikho cha Supa ligi mu chaka cha 2023.
Malipoti omwe tapeza akuonetsa kuti akuluakulu a timuyi ataya chikhulupiliro pa mphunzitsiyu pomwe ati wakanika angakhale kuti anamupatsa zonse zomwe amafuna ngati kumugulira osewera omwe iye amafuna monga Gaddie Chirwa.
Timuyi yati ikulingalira zolemba ntchito mphunzitsi wakale wa Flames, Meke Mwase, kuti atenge ntchitoyi ndipo adikira Harrison kuti amalize mgwirizano wake omwe ukutha mu 2024.
Timuyi inamaliza pa nambala yachitatu pomwe inachepekedwa ndi mapointsi asanu okha basi kuti ifike pomwe panali FCB Nyasa Big Bullets yomwe inatenga chikhochi kachisanu kotsogozana.
OYIMBIRA AKU MALAWI AOMBA M'GOLO
Bungwe la Confederation of African Football latulutsa ndandanda wa oyimbira omwe atumikire mmasewero akumpikisano wa African Cup of Nations womwe uyambe chaka cha mawa.
Mayinawa ndi makumi asanu ndi mmodzi mphambu zisanu ndi zitatu (68) ochokera mmayiko angapo komatu palibepo oyimbira angakhale mmodzi yemwe wasankhidwa kuchokera ku Malawi.
Izi zikudza pomwe tsopano pakutha zaka tsopano oyimbira amdziko lino asakutengedwa ku mipikisano ikuluilkulu pomwenso matimu ochuluka akumadandaula ndi kayimbilidwe ka oyimbirawa mmalawi.
"TAGWIRIZANA KUTI PASUWA ATENGE ZONSE" - MWAMADI
Mkulu wamasapota kutimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Stone Mwamadi, wati timu yawo yakambirana kuti zikho zonse ziwiri zomwe atsala nazo atenge kuti mphunzitsi wawo, Callisto Pasuwa, apange mbiri.
Iye amanena izi patsogolo pa masewero a matimu awiriwa lamulungu pa bwalo la Kamuzu ndipo akuti Maule sangalore kuti kugwako akagwere pa Manoma.
"Kunoko tachita kugwirizana kuti mphunzitsi wathu, Callisto Pasuwa, apange mbiri chifukwa tatenga kale ziwirizo nde izi zatsalazi zikubwera ndithu nde Maule pompaja tikamenye Manoma." Anatero Mwamadi.
Matimuwa akumana mu ndimeyi atakanikana kugonjetsana mmasewero atatu mu chakachi ndipo wopambana akumana ndi wopambana pakati pa Bangwe All Stars komanso Silver Strikers mu ndime yotsiriza.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
"MAULE TIWASWA NGATI WAKUBA" - CHITSULO
Wapampando wa masapota atimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Dennis Chitsulo, wati zopweteka zonse zomwe akhala akukumana nazo ndi FCB Nyasa Big Bullets zitha lamulungu likudzali pomwe ayiponde modetsa nkhawa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero amatimu awiriwa mu ndime ya matimu anayi a chikho cha Castel ndipo wati Manoma akhamukire ku bwalo la Kamuzu kuti akadye nyama.
"Ife tonse tagwirizana kuti uyu yekha tikamumenye pa Kamuzu, sikuti ndi chigoli chimodzi ayi koma mangawa onse akathera pa iyeyu." Anatero Chitsulo.
Matimuwa akamakumana nthawi zambiri, FCB Nyasa Big Bullets ndi imene imapambana ndipo pa masewero atatu omwe akumana, onse alepheranako.
NDIME YOTSIRIZA YA AIRTEL TOP 8 ILIKO PA 6 JANUARY 2024
Bungwe la Football Association of Malawi latulutsa tsiku limene kudzakhala ndime yotsiriza ya mpikisano wa Airtel Top 8 komanso bwalo lomwe lichititse masewerowa.
Malingana ndi bungweli, masewerowa adzakhala pa 06 January 2024 ndipo adzaseweredwa pa bwalo la Bingu ndi matimu a FCB Nyasa Big Bullets komanso wopambana pakati pa Silver Strikers komanso MAFCO.
Mkulu wokonza mipikisano ku bungweli, Gomegzani Zakazaka, wati mmene anakonzera simmene zakhalira malingana ndi milandu ya Mighty Mukuru Wanderers.
"Mmene calendar yathu tinayikira simmene yakhalira chifukwa tachedwabe koma sabata yoyamba ya chaka cha mawa ndi imene tidzamalizitse zonse." Anatero Zakazaka.
Ndime ya matimu anayi pakati pa Silver ndi MAFCO iliko lachiwiri pa 26 December 2023.
"KUKHALA CHETEKO NDEKUTI TIKUFUFUZA" - BANDA
Mlembi wamkulu wabungwe la Super League of Malawi, Williams Banda, wayankhulapo pa kudandaula kwa timu ya Blue Eagles kuti bungweli silikuyankhabe pa dandaulo lawo chifukwa choti likufufuza.
Banda wayankhula izi kutsatira kudandaula kwa Blue Eagles kuti SULOM ikuchedwa kuwayankha koma iye wati angakhale Blue Eagles yomweyo ikudziwa malamulo okhudza nthawi yomwe bungwe lawo likhonza kuwayankhira.
"Dandaulo likafika ndekuti limapita Ku disciplinary komiti yomwe imayenera kuti ifufuze nde kuchedwako sikuti angokhala koma akufufuza. Zokhudza kuti tiyankha liti pali malamulo omwe angakhale a Blue Eagles akuwadziwa komanso inunso mukuwadziwa." Anatero Banda.
Blue Eagles inalembera SULOM kuti ifufuze zachinyengo pakati pa matimu achisilikali a Red Lions komanso Moyale Barracks omwe anathandizira kuti Blue Eagles ituluke mu ligi ya TNM.
"BANGWE INABWERA KUTI IZAGAWE ZIGOLI" - JIKA
Mwini wake watimu ya Bangwe All Stars wati walonjeza anyamata ake zinthu zabwino zomwe adzanene masewero akadzatha zimene zipangitse kuti timuyi ifike ndime yotsiriza ya Castel Challenge Cup.
Iye wayankhula izi patsogolo pa masewero atimuyi ndi Silver Strikers mu ndime ya matimu anayi ampikisanowu ndipo wati timu ya Bangwe inafika mdziko muno kudzagawa zigoli.
"Ndili ndi uthenga wabwino kwa masapota kuti loweruka tikukafika mu ndime yotsiriza. Anyamata tawalonjeza ka 2 kwacha kamphamvu ndikuti akachite bwino ndipo pakutha pa masewero timu yabwino ikapambana." Anatero Jika.
Timu ya Bangwe yakumanako ndi Silver kawiri mu ligi pomwe koyamba anagonja 4-1 ku Lilongwe ndipo anapambana 3-2 pa bwalo la Kamuzu mu chigawo chachiwiri cha ligi.
Wopambana masewerowa adzakumana ndi wopambana pakati pa FCB Nyasa Big Bullets komanso Mighty Mukuru Wanderers mu ndime yotsiriza yomwe opambana adzatenga K50 million.
"SITIKASUMANSO KUTI MPIRA UKOME" - WANDERERS
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yavomereza chigamulo chomwe komiti yoona zamilandu ku bungwe la Football Association of Malawi lapereka kummawa kwa lachinayi ndipo yati sikasumanso kuti mwina mpira uyendenso bwino.
Mu kalata imene timuyi yatulutsa kummawa wa lachinayi yomwe yasainidwa ndi Chancy Gondwe yati timuyi yasankha kuvomereza chigamulo ngakhale imafuna kukasumira bungwe ku Court of Arbitration for Sports.
Iyo yatinso bungweli liunikirenso njira za momwe bungweli limaunikilira milandu kuti akonze zinthu zomwe timuyi sinayankhidwe kuti zisadzachitikenso ndipo yafunira FAM yonse khilisimisi komanso chaka chatsopano chopambana.
Bungweli lauza Wanderers kupereka K22.1 million komanso kuti anatuluka mu chikho cha Airtel Top 8.
CIVO IPEREKA MPHOTO KWA OSEWERA LACHISANU
Timu ya Civo United ili ndi mwambo womwe ikuyenera kupereka mphoto kwa osewera omwe achita bwino mu ligi ya chaka cha 2023 lachisanu kunyumba ya timuyi mu mzinda wa Lilongwe.
Timuyi yakonza mwambowu kuti akakhale ndi madyerero aakulu omaliza amu chaka chino komanso kupereka mphoto kwa osewera omwe anathandiza timuyi kuti asatuluke mu ligi ya TNM
Mwambowu ukubwera nthawi imene osewera atimuyi akufuna timuyi iwapatse ndalama zawo pafupifupi K390,000 ndipo anyamatawa anakavuta kunyumbayi lachiwiri lapitali.
Civo inamaliza pa nambala yachisanu ndi chitatu pomwe inatolera mapointsi 37 pa masewero 30 omwe inasewera mu timuyi.
WANDERERS INATULUKA MU AIRTEL TOP 8
Timu ya Silver Strikers isewera ndi timu ya MAFCO mu ndime ya matimu anayi amuchikho cha Airtel Top 8 pomwe bungwe la Football Association of Malawi lachotsa madando onse atimu ya Mighty Mukuru Wanderers okhudza masewero awo achibwerenza ndi Silver Strikers omwe iwo sanabwere.
Komiti ya bungweli yomva zidandaulo yagamula kuti Wanderers isalipire K2 million pa mlandu onyanyala m'bwalo la za masewero komanso K500,000 kamba kolephera kusungitsa mwambo pakati pa otsatira ake koma zilango zina zonse zikhala momwemo.
Timuyi ilipira K22 million pa zilango zonse za nkhaniyi kuphatikizapo kukonzetsera mipando pa bwalo la Bingu ku Lilongwe komanso kuti anagonja 2-0 ndi Silver Strikers mmasewero achibwerenza.
Matimu a Silver Strikers komanso MAFCO akumana lachiwiri pa 26 December 2023 mu masewero ozigulira malo mu ndime yotsiriza. Wanderers yapezeka yolakwa posabwera mmasewero achibwerezawa komanso ponyanyala masewero oyamba pa bwalo la Bingu.
NKHANI YA FAM NDI WANDERERS ITHA LERO
Mkulu wokonza mipikisano ku bungwe la Football Association of Malawi, Gomegzani Zakazaka, wati nkhani yomwe ili pakati pa Mighty Mukuru Wanderers komanso bungweli ikuyenera kutha lero pomwe komiti ya appeals ipereke chiganizo chomaliza.
Iye amayankhula izi potsimikiza kuti nkhaniyi yokhudza kusuma kwa Wanderers malingana ndi malamulo sidutsanso pamenepa pomwe chiganizo cha lero chikhale chomaliza.
"Tikutsimikiza kuti appeal komiti ikumane lero kuti ipange chiganizo chomaliza chifukwa komitiyi inatsimikiza chiganizo cha komiti ya mpikisanowu koma Wanderers inakasuma ndipo inamvedwa lachitatu sabata yatha nde chiganizo chonse chili lero." Anatero Zakazaka.
Wanderers inasuma pokana chigamulo choti inagonja 2-0 komanso ipereke ndalama zokwana K24.5 million kamba kophwanya mipando pa bwalo la Bingu.
CHAWINGA'S WUHAN CONTRACT EXPIRES
Scorchers forward, Temwa Chawinga, says she is overwhelmed with offers she is receiving from different teams in Europe and China but says she is weighing them.
This comes after the expiry of her four years contract with Wuhan Jiangda this month and has attracted the interests of team's following her brilliant performances in China Women's Super League. She said she is still looking into the offers.
"I am overwhelmed with the offers I am getting from Europe and China. My contract with Wuhan expired but they have offered me a year long to help them in the Asian Champions League and some teams in Europe have reached me so I am weighing the deals." Said Chawinga.
The star had a year to remember after winning four golden boot awards as she scored 61 goals for club and Country in 2023.
CHAWINGA NETS FIRST CHAMPIONS LEAGUE GROUPS GOAL
Scorchers captain, Tabitha Chawinga, produced a remarkable performance after recording her first UEFA Champions League Group stage goal and an assist as PSG claimed an away 3-1 victory against Italian Serie A Champions, AS Roma, on Wednesday night.
Chawinga chipped off the Roman goalkeeper in the first half to give the visitors a lead at half time before assisting her Captain Bartimole, passing the ball where she was tightly marked with five players on 58th minute.
The Parisans then led 3-0 deep in the second half before a late consolation goal from the hosts through a wonderful free kick for PSG to win 3-1.
The team now has 6 points on second position, a point behind Ajax, a point ahead of Roma and two points ahead of Bayern in their group of death and they have to stage a revenge against Ajax and Bayern Munchen.
By Hastings Wadza Kasonga Jr
ALGERIA SUSPENDS FOOTBALL ACTIVITIES AFTER MOULOUDIA ACCIDENT CLAIMING THREE
The Algerian Football Association has suspended all football activities in the country until further notice after an accident involving Mouloudia El Bayadh which has claimed three lives including the team's goalkeeper.
Mouloudia was travelling to fulfill their assignmenton against JS Kabylie on Friday when the accident occurred amd three people have been confirmed dead while four players are seriously injured.
Those who are dead are the team's goalkeeper, Zakaria Bouziani, assistant coach Khaled Moftah and the team's driver.
Meanwhile, the draw for the Algerian Cup scheduled for December 26 has also been shifted to a later date to be communicated by the Association.
BAKA CITY RULES KARONGA
SIMSO and Innobuild Northern Region Football League champions, Baka City, continue to humble giants after beating Karonga United 1-0 in a friendly organized by Willy Yabwanya Phiri at the Karonga United on Wednesday afternoon.
Substitute, Lupakisho Kazingo, needed only 11 minutes to head home two minutes from time to grant the Clever boys a sweet victory in a newly formed Karonga derby.
After a barren 45 minutes, Baka went close through Mwakyembe and Sherrif Shamama whereas Davie Tobias hit the post for Karonga before Kazingo's introduction on 77th minute to seal the win on 88th minute.
In other games, Karonga United Reserve lost 1-0 to Karonga United whereas Karonga United Women beat St Marys Women 3-1 on the same pitch.
CHIKUPIRA STRIKES A DEAL WITH GREEN BUFFALOES
FCB Nyasa Big Bullets forward, Vanessa Chikupira, will play in the FAZ Women's Super League in Zambia after striking a deal with Green Buffaloes, the People's team has confirmed.
Chikupira has penned a one year deal with the team after completing a permanent deal in an disclosed fee with the Zambian side.
She makes the move after helping FCB Nyasa Big Bullets Women to finish second in the FAM Women's League in the Southern Region and was the league's top scorer with 46 goals.
She will join her Scorchers compatriot, Ireen Khumalo, who has penned a deal last week with Buffaloes. She is the third to leave the team this year after Mary Chabvinda who went to Rayon Sports Women in Rwanda and Emily Jossam who joined ZESCO United of Zambia.
BANDA TO POCKET K136 MILLION FROM TANZANIAN DEAL
Malawian talented forward, Peter Banda, is set to return to Tanzania four months after leaving the country's giants, Simba SC, after signing a deal with the country's side, Singida Fountain Gate.
The country's blogger, Micky Jr, confirmed the news on Tuesday saying the deal has already been signed and he will get $80,000 (about K136,000,000) as signing on fee that will be paid in two installments.
Meanwhile, the player confirmed about the news saying they are awaiting the final part of the discussions so that they make an official statement.
Banda re-joined FCB Nyasa Big Bullets where he signed a four months contract and has won the FDH Bank Cup and the TNM Super League with the team.
All the best my idol jemba
Fixture for tomorrow
FAM IPEREKA K0.45 BILLION KWA MEKE MWASE
Bwalo lamilandu ku Blantyre lagamula kuti bungwe la Football Association of Malawi apereke ndalama pafupifupi K450 million kwa mphunzitsi wakale wa Flames, Meke Mwase, kamba kochotsedwa ntchito mopanda lamulo.
Bwaloli lati FAM ilipire Mwase ndalama ngati zomwe amamupatsa Mario Marinica chifukwa iye amapatsidwa K1.3 million pomwe Marinica anapatsidwa K12.9 million ngakhale ntchitoyo ndi imodzi.
Woyimilira pa mlandu kwa Mwase, David Kanyenda, wati ndi wokondwa ndi mmene mlanduwu ukuyendera.
"Bwalo linaunikira bwino nkhani ya malipiro nde apeza kuti zomwe zimachitikazi unali mchitidwe wosalana poti uyu ndi mmalawi amapatsidwa ndalama zochepa." Anatero Kanyenda.
Bwaloli lapeza kuti FAM inalakwitsa kuchotsa Mwase kamba koti analembedwa ndi boma la Malawi osati bungweli ndipo bwaloli lapititsa mlanduwu ku bwalo lalikulu pa nkhani yowachotsa mosakhala bwino komanso kuipitsilidwa mbiri.
Mwase akhala mphunzitsi wachiwiri kuchokera kwa Ernest Mtawal
PHIRI WATENGANSO MPHOTO YACHITATU KU BULLETS
Katswiri yemwe amasewera kumbuyo komanso pakati Ku timu ya FCB Nyasa Big Bullets yapambananso mphoto ya wosewera wapamwamba mu mwezi wa November kutimuyi kutsatira kupeza mavoti ochuluka kwa ochemerera.
Phiri wagonjetsa Patrick Mwaungulu yemwe anapeza mavoti 13 pa anthu 100 aliwonse pomwe Yankho Singo anapeza mavoti 4 pa mavoti 100 ndipo Phiri anasesa mavoti 83 pa anthu 100 aliwonse.
Iye anapambananso mphoto ngati yomweyi mu mwezi wa October komanso November.
HAIYA AKUPITA KU SAUDI ARABIA
Mtsogoleri yemwe wangosankhidwa kumene ku bungwe la Football Association of Malawi, Fleetwood Haiya, anyamuka mdziko muno lachitatu kupita ku Saudi Arabia komwe akakumane ndi mtsogoleri wa bungwe la FIFA, Gianni Infantino.
Mtsogoleriyu waitanidwa ndi Infantino kuti akakambirane naye magawo ena otukula nkhani za masewero mdziko muno ndipo aperekezedwa ndi mlembi wamkulu wa bungweli, Alfred Gunda.
Iwo akakhala nawo pamwambo a mkumano wa FIFA World Cup Championship komanso FIFA Football ndipo akuyembekezeka kubwerera loweruka mdziko muno.
Haiya walowa pa mpandowu loweruka lathali atapeza mavoti okwana 23 kwa 13 pa mtsogoleri wakale wa bungweli, Walter Nyamilandu Manda.
MASEWERO ONSE A CASTEL ALI PA KAMUZU
Bwalo la Kamuzu lichititsa masewero a ndime ya matimu anayi amu chikho cha Castel pomwe bungwe la Football Association of Malawi latulutsa ndandanda wa masiku komanso bwalo lake lolemba masana.
Masewero oyamba aliko loweruka pomwe Silver Strikers ibwerenso ku Blantyre kudzakumana ndi Bangwe All Stars pa bwalo la kamuzu ndipo lamulungu lakelo, FCB Nyasa Big Bullets idzakhala pakhomo kukumana ndi Mighty Mukuru Wanderers mu masewero achiwiri.
Opambana mmasewero onsewa adzakumana mu ndime yotsiriza ya mpikisanowu ndipo wopambana adzapeza ndalama zokwana K50 million. Umu ndi mmene zitakhalire:
LOWERUKA, 23 DECEMBER 2023 โขBangwe All Stars vs Silver Strikers
LAMULUNGU, 24 DECEMBER 2023 โขFCB Nyasa Big Bullets vs Mighty Mukuru Wanderers
Reported by Hastings Wadza Kasonga Jr
Chipiku log table 2023
"TATHANA NDI UMUGABE" - VINGULA CONGRATULATES HAIYA
One of the people who were interested in vying for Football Association of Malawi's Presidency, Balawala Vingula, has expressed his happy attitude after seeing the current President, Fleetwood Haiya, defeating Walter Nyamilandu Manda for the position.
Vingula labelled the former President as Mugabe for his 19 year stay at the Association and hish to serve for another term and then wished Haiya well as he works for the next four years.
"Tathana ndi Umugabe! Receive my congratulations on our Victory as a country by electing you as Our FAM President. I hope that God will not deny you Wisdom. All the best FH." Wrote Vingula.
Vingula showed his interested to stand for the position in 2019 and 2023 but he did not receive any nomination in both Elections.
MKANDAWIRE WAYAKA MOTO KU ZAMBIA
Katswiri wosewera mpira wamiyendo koma ali mzimayi wa mdziko muno, Mercy Vitumbiko Mkandawire, akupitiliza kuchita bwino mdziko la Zambia pomwe tsopano ali ndi zigoli zisanu ndi zitatu mu ligi ya mdzikomo.
Mkandawire anagoletsa zigoli ziwiri lamulungu pomwe timu yake ya ZISD inagonjetsa Chipata Blue Eagles Ladies 5-0 mu FAZ Women's Super League kuti apitilize kuchita bwino mu ligiyi.
Iyenso wakwanitsa kuthandizira zigoli zisanu ndi ziwiri (7) zomwe zikuonetsa kuti akukhudzidwa ndi zigoli 15 mu ligiyi.
Iye amatha kusewera ngati womwetsa zigoli kapenanso mmbali chakutsogolo pomwe ndi mmodzi mwa osewera omwe ali ndi liwiro kwambiri.