NDIME YOTSIRIZA YA AIRTEL TOP 8 ILIKO PA 6 JANUARY 2024
Bungwe la Football Association of Malawi latulutsa tsiku limene kudzakhala ndime yotsiriza ya mpikisano wa Airtel Top 8 komanso bwalo lomwe lichititse masewerowa.
Malingana ndi bungweli, masewerowa adzakhala pa 06 January 2024 ndipo adzaseweredwa pa bwalo la Bingu ndi matimu a FCB Nyasa Big Bullets komanso wopambana pakati pa Silver Strikers komanso MAFCO.
Mkulu wokonza mipikisano ku bungweli, Gomegzani Zakazaka, wati mmene anakonzera simmene zakhalira malingana ndi milandu ya Mighty Mukuru Wanderers.
"Mmene calendar yathu tinayikira simmene yakhalira chifukwa tachedwabe koma sabata yoyamba ya chaka cha mawa ndi imene tidzamalizitse zonse." Anatero Zakazaka.
Ndime ya matimu anayi pakati pa Silver ndi MAFCO iliko lachiwiri pa 26 December 2023.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores