WANDERERS IKUKAMBIRANA NDI CHESTER
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yatsegula zokambirana ndi katswiri wawo wakale, Yamikani Chester, kuti abwererenso kutimuyi mgwirizano wake ukatha ku timu ya Coastal do Sol yaku Mozambique.
Chester anachoka ku Wanderers kumayambiliro a chaka chino atakanika kumvana ndi timuyi ndipo anasaina mgwirizano wa chaka chimodzi ku Mozambique komwe amachita bwinonso kwambiri.
Koma zamveka kuti katswiriyu sakufunanso kubwereranso ku dzikoli ndipo Manoma akufuna atatemganso ma busy.
Timuyi ikukambirananso ndi wosewera wa Civo, Lloyd Aaron, yemwe malipoti akuonetsa kuti mmodzi mwa aphunzitsi ku Flames anamuuza kuti asapite ku Wanderers poti samasamala osewera bwino komanso Clement Nyondo wa Dedza Dynamos yemwe akuopa kuti atha kumakangokhala panja Ku Nomaku.
Apite bass Mr bus
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores