"SITIKASUMANSO KUTI MPIRA UKOME" - WANDERERS
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yavomereza chigamulo chomwe komiti yoona zamilandu ku bungwe la Football Association of Malawi lapereka kummawa kwa lachinayi ndipo yati sikasumanso kuti mwina mpira uyendenso bwino.
Mu kalata imene timuyi yatulutsa kummawa wa lachinayi yomwe yasainidwa ndi Chancy Gondwe yati timuyi yasankha kuvomereza chigamulo ngakhale imafuna kukasumira bungwe ku Court of Arbitration for Sports.
Iyo yatinso bungweli liunikirenso njira za momwe bungweli limaunikilira milandu kuti akonze zinthu zomwe timuyi sinayankhidwe kuti zisadzachitikenso ndipo yafunira FAM yonse khilisimisi komanso chaka chatsopano chopambana.
Bungweli lauza Wanderers kupereka K22.1 million komanso kuti anatuluka mu chikho cha Airtel Top 8.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores