NKHANI YA FAM NDI WANDERERS ITHA LERO
Mkulu wokonza mipikisano ku bungwe la Football Association of Malawi, Gomegzani Zakazaka, wati nkhani yomwe ili pakati pa Mighty Mukuru Wanderers komanso bungweli ikuyenera kutha lero pomwe komiti ya appeals ipereke chiganizo chomaliza.
Iye amayankhula izi potsimikiza kuti nkhaniyi yokhudza kusuma kwa Wanderers malingana ndi malamulo sidutsanso pamenepa pomwe chiganizo cha lero chikhale chomaliza.
"Tikutsimikiza kuti appeal komiti ikumane lero kuti ipange chiganizo chomaliza chifukwa komitiyi inatsimikiza chiganizo cha komiti ya mpikisanowu koma Wanderers inakasuma ndipo inamvedwa lachitatu sabata yatha nde chiganizo chonse chili lero." Anatero Zakazaka.
Wanderers inasuma pokana chigamulo choti inagonja 2-0 komanso ipereke ndalama zokwana K24.5 million kamba kophwanya mipando pa bwalo la Bingu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores