CIVO IPEREKA MPHOTO KWA OSEWERA LACHISANU
Timu ya Civo United ili ndi mwambo womwe ikuyenera kupereka mphoto kwa osewera omwe achita bwino mu ligi ya chaka cha 2023 lachisanu kunyumba ya timuyi mu mzinda wa Lilongwe.
Timuyi yakonza mwambowu kuti akakhale ndi madyerero aakulu omaliza amu chaka chino komanso kupereka mphoto kwa osewera omwe anathandiza timuyi kuti asatuluke mu ligi ya TNM
Mwambowu ukubwera nthawi imene osewera atimuyi akufuna timuyi iwapatse ndalama zawo pafupifupi K390,000 ndipo anyamatawa anakavuta kunyumbayi lachiwiri lapitali.
Civo inamaliza pa nambala yachisanu ndi chitatu pomwe inatolera mapointsi 37 pa masewero 30 omwe inasewera mu timuyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores