"BANGWE INABWERA KUTI IZAGAWE ZIGOLI" - JIKA
Mwini wake watimu ya Bangwe All Stars wati walonjeza anyamata ake zinthu zabwino zomwe adzanene masewero akadzatha zimene zipangitse kuti timuyi ifike ndime yotsiriza ya Castel Challenge Cup.
Iye wayankhula izi patsogolo pa masewero atimuyi ndi Silver Strikers mu ndime ya matimu anayi ampikisanowu ndipo wati timu ya Bangwe inafika mdziko muno kudzagawa zigoli.
"Ndili ndi uthenga wabwino kwa masapota kuti loweruka tikukafika mu ndime yotsiriza. Anyamata tawalonjeza ka 2 kwacha kamphamvu ndikuti akachite bwino ndipo pakutha pa masewero timu yabwino ikapambana." Anatero Jika.
Timu ya Bangwe yakumanako ndi Silver kawiri mu ligi pomwe koyamba anagonja 4-1 ku Lilongwe ndipo anapambana 3-2 pa bwalo la Kamuzu mu chigawo chachiwiri cha ligi.
Wopambana masewerowa adzakumana ndi wopambana pakati pa FCB Nyasa Big Bullets komanso Mighty Mukuru Wanderers mu ndime yotsiriza yomwe opambana adzatenga K50 million.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores