"MAULE TIWASWA NGATI WAKUBA" - CHITSULO
Wapampando wa masapota atimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Dennis Chitsulo, wati zopweteka zonse zomwe akhala akukumana nazo ndi FCB Nyasa Big Bullets zitha lamulungu likudzali pomwe ayiponde modetsa nkhawa.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero amatimu awiriwa mu ndime ya matimu anayi a chikho cha Castel ndipo wati Manoma akhamukire ku bwalo la Kamuzu kuti akadye nyama.
"Ife tonse tagwirizana kuti uyu yekha tikamumenye pa Kamuzu, sikuti ndi chigoli chimodzi ayi koma mangawa onse akathera pa iyeyu." Anatero Chitsulo.
Matimuwa akamakumana nthawi zambiri, FCB Nyasa Big Bullets ndi imene imapambana ndipo pa masewero atatu omwe akumana, onse alepheranako.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores