"TAGWIRIZANA KUTI PASUWA ATENGE ZONSE" - MWAMADI
Mkulu wamasapota kutimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Stone Mwamadi, wati timu yawo yakambirana kuti zikho zonse ziwiri zomwe atsala nazo atenge kuti mphunzitsi wawo, Callisto Pasuwa, apange mbiri.
Iye amanena izi patsogolo pa masewero a matimu awiriwa lamulungu pa bwalo la Kamuzu ndipo akuti Maule sangalore kuti kugwako akagwere pa Manoma.
"Kunoko tachita kugwirizana kuti mphunzitsi wathu, Callisto Pasuwa, apange mbiri chifukwa tatenga kale ziwirizo nde izi zatsalazi zikubwera ndithu nde Maule pompaja tikamenye Manoma." Anatero Mwamadi.
Matimuwa akumana mu ndimeyi atakanikana kugonjetsana mmasewero atatu mu chakachi ndipo wopambana akumana ndi wopambana pakati pa Bangwe All Stars komanso Silver Strikers mu ndime yotsiriza.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores