HAIYA AKUPITA KU SAUDI ARABIA
Mtsogoleri yemwe wangosankhidwa kumene ku bungwe la Football Association of Malawi, Fleetwood Haiya, anyamuka mdziko muno lachitatu kupita ku Saudi Arabia komwe akakumane ndi mtsogoleri wa bungwe la FIFA, Gianni Infantino.
Mtsogoleriyu waitanidwa ndi Infantino kuti akakambirane naye magawo ena otukula nkhani za masewero mdziko muno ndipo aperekezedwa ndi mlembi wamkulu wa bungweli, Alfred Gunda.
Iwo akakhala nawo pamwambo a mkumano wa FIFA World Cup Championship komanso FIFA Football ndipo akuyembekezeka kubwerera loweruka mdziko muno.
Haiya walowa pa mpandowu loweruka lathali atapeza mavoti okwana 23 kwa 13 pa mtsogoleri wakale wa bungweli, Walter Nyamilandu Manda.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores