Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
Games today
Fixtures
BAKA CITY YATENGA CHIKHO CHACHITATU MU 2023
Timu yomwe yangolowa kumene mu TNM supa ligi ya Baka City tsopano yakwanitsa kutenga zikho zitatu mu chaka cha 2023 pomwe yakhala akatswiri a chikho cha Nyasa Capital Finance chakumpoto atagonjetsa Iponga FC 1-0 mu ndime yotsiriza lamulungu.
Eddie Mwangama anagoletsa chigoli chokhacho pa mphindi zinayi za masewero omwe kuti timuyi ikhale akatswiri.
Ichi ndi chikho chachitatu chaka chino atatenga Mayors Trophy Ku Tanzania my mwezi wa July komwe anagonjetsa matimu amu dzikoli ndipo atenganso ukatswiri wa ligi yakumpoto yomwe yawatengera mu Supa ligi.
The Clever Boys ikuyang'ananso zotenganso chachinayi pomwe akumane ndi Wanderers Reserve mu ndime ya matimu anayi mu King Kabvina Trophy ku Dowa.
BAKA CITY WINS THE NYASA CAPITAL FINANCE CUP
Karonga based side, Baka City, are the BAKA CITY WINS THE NYASA CAPITAL FINANCE CUP
Karonga based side, Baka City, are the Champions of the Northern Region Nyasa Capital Finance Cup after beating Iponga FC 1-0 on Sunday afternoon in the final.
Eddie Mwambungu powered in a thundering header on 4th minute of the game to seal the victory.
Its now three trophi of the Northern Region Nyasa Capital Finance Cup after beating Iponga FC 1-0 on Sunday afternoon in the final.
Its now three trophies this year for the Clever boys after winning the Northern Region SIMSO and Innobuild Football league that saw them promoted into the Super League and also a Trophy in Tanzania earlier this year.
Last week, the team knocked out FCB Nyasa Big Bullets in the King Kabvina Trophy in Dowa to reach the semi finals where they will play Mighty Mukuru Wanderers Reserve.
Fixture nyasa big bullets and might wandarazi
Maule more fire
Results nyasa big bullets and might wandarazi
Games
Kodi log table ilikuti?
NYAMILANDU WAFUNIRA ZABWINO HAIYA
Mtsogoleri yemwe wangochoka kumene Ku Football Association of Malawi, Walter Nyamilandu Manda, wamufunira zabwino yemwe walowa mmalo mwake, Fleetwood Haiya, pamene akuyamba kugwira ntchito yake.
Iye walankhula izi kudzera mu kalata yake atagonja pa zisankhozi ndipo iye wati ndi wokondwa poti akuchoka mpira ulibwino kusiyana ndi mmene anaupezera.
Iye wathokoza amalawi polora kuti atsogolere mpira wamiyendo mdziko muno pomwe anakwanitsa kupanga zinthu zingapo zobweretsa chimwemwe kwa amalawiwa.
Haiya wakhala woyamba kuchotsa Nyamilandu yemwe anayamba kulamulira kuchokera mu chaka cha 2004.
CHAMPIONS BULLETS LEAD SUPER LEAGUE TEAMS IN CINGRATULATING HAIYA
TNM Super League Champions, FCB Nyasa Big Bullets, has lead the other 15 teams in congratulating the outgoing Super League of Malawi President, Fleetwood Haiya, for his landslide victory in the Football Association of Malawi Presidency Election on Saturday.
Haiya beat Former FAM President, Walter Nyamilandu Manda, with 23 votes to 13 in Mzuzu to claim the hot seat at the Mpira house and teams have congratulatulated him for the Victory.
Relegated side, Extreme FC became the first team to react to the victory with the Chichewa word 'Amubaya' then Silver Strikers, Bangwe All Stars, Dedza Dynamos, Moyale Barracks and Civo United followed.
Haiya has served as the SULOM for one year after knocking out Tiya Somba Banda last year and now the body will be lead by Major Gilbert Mitawa, who was his vice.
Bkodi mawa kuli game yanji
Games for today
MANOMA NDI MABANKER AKAGOGODANSO KU CIVO
Matimu a Mighty Mukuru Wanderers komanso Silver Strikers alowa nnawo mu gulu lofuna katswiri watimu ya Civo United, Lloyd Aaron, kuti amugule.
Matimuwa adzidzimuka ataona kuti Bullets yapempha Civo kuti iwagulitse katswiriyu pomwe iwo ndi omwe anaonetsa chidwi chachikulu chotenga katswiriyu wa Flamesyu.
Izi zipangitsa kuti malonda a katswiriyu avute pomwe Civo iziyendera tsopano komwe akhuthula ndalama zambiri ndipo katswiriyu anali pa K15 million mphamvu ya kwacha isanagwe.
"KODI ZIKUFUNIKA KUTI MAKOCHI TIZIKALOWA M'BWALO?" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wadandaula kuti timu yake inangopereka zigoli pomwe tsopano timuyi yatuluka mu chikho cha Castel atagonja 4-2 ndi Silver Strikers.
Kananji amayankhula atatha masewerowa ndipo wati sakudziwano kuti osewera aziwayankhula motani chifukwa akumachita zosiyana ndi zomwe akuuzidwa ngakhale timu yawo ikumasewera bwino.
"Tivomereze tagonja 4-2 ndi timu ya Silver Strikers, chibwana chimalanda olo mutatenga CR Socials zigoli zomwe tachititsa lero sangachinyitse, tangopereka zigoli nde zikumadabwitsa kuti mwina tizikalowa makochi m'bwalomo chifukwa kuwauza sindikudziwa kuti akuganiza bwanji akumapanga zina." Anatero Kananji.
Zateremu timuyi tsopano yamaliza chaka cha 2023 ndipo ayamba kukonzera umoyo wawo mu ligi yaying'ono ya Chipiku Stores ya chigawo chapakati atatuluka mu ligi ya TNM.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
"CHANZERU NDI KUWINA OSATI KUMENYA BWINO" - M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wati ndi zabwino kuti timu yake yapitilira mu mpikisano wa Castel Challenge Cup ndipo zoti sanamenye bwino sizofunikira kwambiri.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 4-2 pa bwalo la Bingu lachitatu ndipo wati timu yake inachilimika angakhale kuti simasewera bwino mmasewerowa.
"Tinayamba movutika kwambiri ndipo anzathuwa anatichinya komabe anyamata anayesetsa mpaka tinatsogola kenako kachibwana tinapangitsa penate koma mphunzitsi kopumulira anawayankhula osewera ndipo agwiradi ntchito." Anatero M'gangira.
Iye wati timu yake ichita chothekera kuti mipikisano iwiri ya Airtel Top 8 komanso Castel yomwe ali mu ndime ya matimu anayi atengeko mwina chimodzi kapena zonse. Zateremu, timuyi ikumana ndi Bangwe All Stars mu ndime ya matimu anayi.
"CHIGOLI ANAWANGOWAPATSA A BULLETS CHINATIBALALITSA" - CHIRAMBO
Mphunzitsi watimu ya Ekwendeni Hammers, Elias Chirambo, wati chigoli chomwe FCB Nyasa Big Bullets inapeza choyamba mmasewero omwe matimuwa anakumana chinali chongowapatsa ndipo chinasokoneza osewera ake.
Iye wayankhula izi atatha masewero omwe agonja 4-0 pa bwalo la Kamuzu kuti atuluke mu chikho cha Castel ndipo wati izi ndi kamba koti chigoli choyamba chinali chabodza.
"Masewero anali abwinobwino ndipo timasewera bwino koma chigoli choyamba cha Bullets anangowapatsa nde chinawakhumudwitsa anyamata anga. Ndi osewera ambiri oti amasewera timu yathu yaing'ono nde nzovuta kusewera ndi Bullets ndikumawapatsa zigoli chonchi." Anatero Chirambo.
Zigoli ziwiri za Hassan Kajoke ndi chimodzi aliyense cha Patrick Mwaungulu ndi Precious Sambani ndi zomwe zathandizira kuti Bullets ipitilire mu ndime Ina. Zateremu, Hammers yamaliza chaka chino ndipo ipita kopumulira.
"I WANT MY PLAYERS NOT TO BE FAVOURED BUT PROTECTED" - PASUWA
FCB Nyasa Big Bullets head coach, Callisto Pasuwa, says his players are not protected by the referees in their matches and this is leading to too much injuries to their side.
He said this after their 4-0 victory over Ekwendeni Hammers in the Quarter finals of the Castel Challenge Cup at the Kamuzu Stadium and ahead of the big Blantyre derby, he said his players needs to be protected.
"I am now becoming worried because my players are not protected, you see in each and every game we are losing players, it's now 10 players imagine and today we have changed two players, not even a yellow card so I don't want to be favoured no but they have to be protected." Said Pasuwa.
In the match, Maxwell Gasten Phodo was replaced by Peter Banda on 62nd minute due to an injury after he was fouled in the box but the referee had no interest while Ephraim Kondowe spent just 7 minutes in the pitch and Stanley Biliati replaced him for a knock.
BULLETS YAMVANA NDI AARON
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yamvana ndi katswiri wapakati wa Civo United, Lloyd Aaron, kuti akatumikire timuyi chaka cha mawa ndipo Bullets yalembera kalata Civo kupempha ntchito za katswiriyu.
Bullets yalemba kuti ikusungira K3 million pa mnyamatayu ndikuti akhonza kuwapatsakonso osewera ena ngati mbali imodzi ya malondawa.
Pamene tinkapumulira ligi, katswiriyu anafunidwapo ndi matimu a Mighty Mukuru Wanderers komanso Silver Strikers ndipo Civo inati K15 million ndi yomwe amafuna pa katswiriyu.
supporting mighty wonderers as the best team and wisdom mpinganjira as the best player
"TIKUYANG'ANA CASTEL NDIPO AMENEYU TIMWA NDITHU" - KANANJI
Mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Eliya 'Carlsberg Cup' Kananji, wati timu ya Blue Eagles sipita mophweka pomwe akukumana ndi timu ya Silver Strikers mu chikho cha Castel ndipo wati timu yonse ikuyang'ana pa chikho chomwechi.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewerowa pa bwalo la Bingu lachitatu ndipo wati timu ya Silver Strikers isapite moderera kuti iwo anatuluka kamba koti apita ndi mtima onse.
"Ndi masewero ovuta kwambiri ndipo anzathuwo asabwere mophweka kuti mwina poti tinatuluka mu ligi koma kukubwera January anyamata akufunikira ka ndalama koti atuluke nako nde ife maso athu ali pamenepa Castel ameneyu timwa ndithu." Anatero Kananji.
Iye wati anyamata ake anachivomera zoti atuluka mu ligi ndipo onse chidwi chili pa masewero amenewa. Omwe apambane mmasewero amenewa adzakumana ndi Bangwe All Stars mu ndime ya matimu anayi.
MWAUNGULU WACHIRA NDIPO ASEWERA NDI EKWENDENI
Katswiri mbambande wa timu ya FCB Nyasa Big Bullets, Patrick Mwaungulu, akuyembekezeka kuonedwanso pa bwalo la zamasewero lachitatu atasowa kwa sabata imodzi pomwe tsopano wachira pa kuvulala kwake.
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimuyi, Heston Munthali, watsimikiza za kubwereranso kwa mnyamatayu patsogolo pa masewero awo ndi Ekwendeni Hammers mu ndime ya matimu asanu ndi atatu a Castel ndipo wati anyamata onse akonzeka.
"Tikukumana ndi timu ya Ekwendeni yomwe titakumana mu ligi chapompano tinavutika nayo ndekuti akhala masewero ovuta kwambiri koma anyamata tawauza kufunikira kwa masewerowa kuti tikawamaliziretu kuti tipite chitsogolo nde takonzeka." Anatero Munthali.
Iye watinso anthu asaikiretu kuti Bullets yadutsa kale mmasewerowa poti masewero amu chikho amakhala ovuta kwambiri. Opambana pa masewerowa akuyembekezeka kukumana ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers mu ndime ya matimu anayi.
KHUMALO WAPITA KU ZAMBIA
Katswiri wotseka kumbuyo kutimu ya Scorchers komanso Silver Strikers Ladies, Ireen Khumalo, akuyembekezeka kukhala wosewera wa Green Buffaloes kwa chaka chimodzi pomwe wasaina mgwirizano pangongole kutimuyi.
Timu ya Silver Strikers yatsimikiza za nkhaniyi kudzera pa tsamba lawo la mchezo lachiwiri kuti katswiriyu akatumikira tsopano mu FAZ Women's Super league ku Zambia.
Iye anapita ku Silver Strikers chaka chomwe chino kuchokera ku Ascent Academy ndipo wakhala ofunikira kwambiri mu ligi ya chaka chino kutimuyi pomwe ali pa nambala yachitatu pambuyo pa MDF Lioness ndi Ascent Academy.
Iye analinso mu gulu la osewera omwe anatenga ukatswiri ndi timu ya Scorchers wa COSAFA Women's Championship mmiyezi yapitayo.
Log table
Castle cup
πThe winners of this yearβs Africa CAF Awards 2023
βοΈ Best player (Victor Osimhen π³π¬) βοΈBest female player (Asisat Oshoala π³π¬) βοΈ Best technical director for men (Walid Regragui π²π¦) βοΈBest womenβs manager (Desiree Ellis πΏπ¦) βοΈ Best goalkeeper (Yassine Bounou π²π¦) βοΈBest goalkeeper female (Chiamaka Nnadozi π³π¬) βοΈ Best goal (Mahmoud Kahraba πͺπ¬) βοΈ Best menβs national team (Morocco π²π¦) βοΈBest womenβs national team (Nigeria π³π¬) βοΈ Best young player (Lamine Kamara πΈπ³) βοΈ Best young player female(Nesryne El Chad π²π¦) βοΈBest player in Africa (Percy Tau πΏπ¦) βοΈ The best player in Africa (Fatima Tagnant π²π¦) βοΈ Best menβs team (Al-Ahly πͺπ¬) βοΈ Best womenβs team (Mamelodi Sundowns πΏπ¦)
Nigerian striker, Victor Osimhen has won the CAF 2023 Menβs Player of The Year award.
He saw off competition from Senegalβs Sadio Mane, and Egyptβs Mohamed Salah, among others.