MKANDAWIRE WAYAKA MOTO KU ZAMBIA
Katswiri wosewera mpira wamiyendo koma ali mzimayi wa mdziko muno, Mercy Vitumbiko Mkandawire, akupitiliza kuchita bwino mdziko la Zambia pomwe tsopano ali ndi zigoli zisanu ndi zitatu mu ligi ya mdzikomo.
Mkandawire anagoletsa zigoli ziwiri lamulungu pomwe timu yake ya ZISD inagonjetsa Chipata Blue Eagles Ladies 5-0 mu FAZ Women's Super League kuti apitilize kuchita bwino mu ligiyi.
Iyenso wakwanitsa kuthandizira zigoli zisanu ndi ziwiri (7) zomwe zikuonetsa kuti akukhudzidwa ndi zigoli 15 mu ligiyi.
Iye amatha kusewera ngati womwetsa zigoli kapenanso mmbali chakutsogolo pomwe ndi mmodzi mwa osewera omwe ali ndi liwiro kwambiri.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores