WANDERERS INATULUKA MU AIRTEL TOP 8
Timu ya Silver Strikers isewera ndi timu ya MAFCO mu ndime ya matimu anayi amuchikho cha Airtel Top 8 pomwe bungwe la Football Association of Malawi lachotsa madando onse atimu ya Mighty Mukuru Wanderers okhudza masewero awo achibwerenza ndi Silver Strikers omwe iwo sanabwere.
Komiti ya bungweli yomva zidandaulo yagamula kuti Wanderers isalipire K2 million pa mlandu onyanyala m'bwalo la za masewero komanso K500,000 kamba kolephera kusungitsa mwambo pakati pa otsatira ake koma zilango zina zonse zikhala momwemo.
Timuyi ilipira K22 million pa zilango zonse za nkhaniyi kuphatikizapo kukonzetsera mipando pa bwalo la Bingu ku Lilongwe komanso kuti anagonja 2-0 ndi Silver Strikers mmasewero achibwerenza.
Matimu a Silver Strikers komanso MAFCO akumana lachiwiri pa 26 December 2023 mu masewero ozigulira malo mu ndime yotsiriza. Wanderers yapezeka yolakwa posabwera mmasewero achibwerezawa komanso ponyanyala masewero oyamba pa bwalo la Bingu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores