MARK HARRISON ALI PA MPENI
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers ikulingalira zochotsa mphunzitsi wawo, Mark Harrison, kuti abwerere pa udindo wake ngati technical director kamba kokanika kutengetsa chikho cha Supa ligi mu chaka cha 2023.
Malipoti omwe tapeza akuonetsa kuti akuluakulu a timuyi ataya chikhulupiliro pa mphunzitsiyu pomwe ati wakanika angakhale kuti anamupatsa zonse zomwe amafuna ngati kumugulira osewera omwe iye amafuna monga Gaddie Chirwa.
Timuyi yati ikulingalira zolemba ntchito mphunzitsi wakale wa Flames, Meke Mwase, kuti atenge ntchitoyi ndipo adikira Harrison kuti amalize mgwirizano wake omwe ukutha mu 2024.
Timuyi inamaliza pa nambala yachitatu pomwe inachepekedwa ndi mapointsi asanu okha basi kuti ifike pomwe panali FCB Nyasa Big Bullets yomwe inatenga chikhochi kachisanu kotsogozana.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores