"PALIBE YEMWE ANADEDWA NDI OYIMBIRA" - KALICHERO
Mlembi wamkulu wa bungwe la oyimbira, Chris Kalichero, wati palibe woyimbira yemwe amadana ndi munthu aliyense pa matimu amu ligi ya TNM koma iwo amangogwira ntchito yawo moyenerera.
Kalichero wayankhula izi pomwe mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter De Jongh, ananena kuti woyimbira Mayamiko Kanjere ali ndi zifukwa zakezake zomwe anamupatsira chikalata chofiira pa masewero omwe timu yake inagonja 1-0 ndi Mighty Mukuru Wanderers pa bwalo la Kamuzu.
Koma Kalichero wati palibe woyimbira yemwe amadana ndi munthu ndipo aliyense amene azifuna kusokoneza masewero azilandira zilango zake.
"Munthu sangapite kukangodana ndi munthu, ife timangogwira ntchito yathuyo, ngati palibepo khalidwe zimene zija zimatsatira." Anatero Kalichero.
Timu ya Silver inalandira makalatawa anayi pomwe wosewera wawo, Nickson Mwase, wachiwiri kwa mphunzitsi, Peter M'gangira ndi wophunzitsa magoloboyi, Sibusiso Padambo, analandiranso awo.