MABEDI AKUFUNIDWA KU SOUTH AFRICA
Mphunzitsi wogwirizira watimu ya Flames, Patrick Mabedi, wati chitsogolo chake ndi chosadziwika bwinobwino pomwe matimu ena amdziko la South Africa akumufuna kuti akaphunzitse kumeneko.
Mgwirizano wa mphunzitsiyu utha mmwezi wa September ndipo iye wati zili ndi bungwe la Football Association of Malawi kuonjezera mgwirizano wake.
"Zonse zili mmanja mwa FAM komano chitsogolo sichikudziwikabe chifukwa matimu ena amu PSL akundifunanso nde tidikirabe ku likuluko." Anatero Mabedi.
Mphunzitsiyu yemwe waphunzitsapo matimu ena ngati Kaizer Chiefs komanso Moloka Swallows ku South Africa, anatenga timu ya Flames mu mwezi wa June kutsatira kutha kwa mgwirizano wa Mario Marinica.
Iye watsogolera Flames mmasewero asanu ndi awiri (7) ndipo sanagonjepo pa mphindi 90 za mkati mwa masewero.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores