"TINGOYANG'ANA CHITSOGOLO POTI IZI ZAPITA" - CHIMODZI JR
Mmodzi mwa akuluakulu ophunzitsa timu ya Silver Strikers, Young Chimodzi Junior, wakana kunena kuti kupatsidwa zikalata zinayi zofiira kutimu yake kunathandizira kuti agonje pomwe timuyi imasewera ndi Mighty Mukuru Wanderers lachinayi pa bwalo la Kamuzu.
Chimodzi amayankhula izi atatha masewero awo ndipo anakana kuthilira ndemanga pa mmene oyimbira Mayamiko Kanjere amaperekera zikalatazi ponena kuti samamva mmene amayankhulirana.
" Mwina tonse timaonera mpira wa kunja, mphunzitsi kukafunsa ziganizo sizolakwika koma ndisayankhule zambiri poti sindikudziwa mmene amayankhulirana komanso tinali ndi mipata yomwe tikanayigwiritsa ntchito izizi sizikanatikhudza." Anatero Chimodzi.
Iye wati ayang'anabe kutsogolo kuti masewero omwe atsala nawo apambane pomwe akuti timu yawo ikadalibe ndi mwayi waukulu kuti ifikire kumtunda.
Timuyi ili pa nambala yachiwiri mu ligi pomwe yapata mapointsi 25 pa masewero 12 omwe yasewera.
Ref sanaimbired bwino
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores