ADELEKE KOLAWOLE WABWERERA KU WANDERERS
Osewera yemwe anachotsedwa chaka Chatha ku timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Adeleke Kolawole, wabwerera kutimuyi ndipo wayamba zokonzekera malinga ndi tsamba la Wa mpira.
Katswiriyu wakhala akusowa kutimuyi kuyambira chaka chatha pomwe anali kuvulalavulala ndipo chimenechi chinali chifukwa chimene timuyi inamuika pa gulu la osewera khumi omwe anachotsedwa kumayambiriro a chaka chino.
Koma mu ndandanda wa osewera omwe timuyi inawalembetsa kuti agwiritsidwa ntchito mu chaka chino, katswiriyu anatchulidwapo koma sanapezeke ndi timuyi mpaka sabata 14 ya ligiyi.
Osewerayu akhonza kuyamba kusewera tsopano pomwe ndi olembetsedwa kale. Osewera monganso Balikinho Mwakanyongo anabwereranso kutimuyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores