Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
MABEDI HAPPY WITH FLAMES' UNBEATEN IN 90 MINUTES
Malawi National Football team caretaker coach, Patrick Mabedi, has praised his boys for a brilliant performance at the COSAFA Cup in South Africa despite finishing fourth in the tournament.
The team lost 5-3 on penalties in the third place match after Christopher Kumwembe missed his penalty against South Africa. Meanwhile, the team has never lost a match in 90 minutes as their defeats in the Semi finals and third place have come through penalties to the delightfulness of Mabedi.
"If it was a league we could have been crowned Champions because we haven't lost a match. I am very proud of my boys we will come back stronger." Mabedi said.
The team finished as group winners in their group after amassing 9 points from three wins but lost to Lesotho 3-0 on penalties after a 1-1 draw in the 90 minutes and also lost to South Africa on Sunday through penalties as well.
Thanks Patrick u did it well n congratulations for that ,the team is gud now just teach them how to shoot π« penalties
DE JONGH AKUFUNA KATINJI
Osewera wakale watimu ya Silver Strikers, Binwell Katinji, akhonza kubwereranso kutimuyi pomwe timuyi yadyerera maso pa katswiriyu kamba ka kuchita bwino kwake.
Katinji wakhala osewera odalilika chaka chino pomwe wagoletsa zigoli zisanu ndi zinayi (9) mipikisano yonse kutimuyi ndipo izi zapangitsa kuti amufune zomutenga.
Iye wasewerapo Silver mmbuyomu pomwe analowera ku Eswatini koma atabweranso, anamukana ndipo anakapeza malo ku Civo. Ngati zingatheke bwinobwino, osewerayu akhale akukaphunzitsidwa ndi Peter De Jongh.
RED CARD INAPITA KOLAKWIKA, YELLOW CARD POKUMWA MADZI ANZAKE
Oyimbira pa masewero a Blue Eagles ndi Karonga United, Brighton Gwiricho anapereka chikalata chofiyira kwa osewera olakwika pomwe anatulutsa Franco Ndawa Jnr mmalo mwa Andrew Juvinala pomwe anamugweba Josiah Duwa wa Karonga United.
Ndawa anadandaulirabe oyimbirayu komatu anatulukabe pomwe Eagles inatsiliza ndi anyamata ochepa mu masewerowa.
Mu chiganizo chinanso, oyimbirayu anapereka kalata ya chikasu kwa osewera wa Karonga United pomwe anamwa madzi a goloboyi wa Blue Eagles, Chakonda Majanga mmasewerowa.
Chigoli cha Josiah Duwa kudzera pa penate ndi chomwe chinapambanitsa timu ya Karonga 1-0 kuti afike pa nambala 7 ndi mapointsi 17 pomwe Eagles ili pa 10 ndi ma points 15.
π COSAFA CHAMPIONS!
Zambia have been crowned COSAFA Cup Champions after defeating Lesotho 1-0 courtesy of a Moyela Libamba goal.
The Chipolopolo have now defended the COSAFA Cup and won the competition for a record-breaking 7th time.
Results
More π₯π₯π₯π₯π₯π₯maule
Mofaya mofaya manoma tonse mon mon
Sabata ino, tapereka ma K5,000 kwa Ernesto ndi Juvencio ndipo tayamba kupereka ma K1,667 kwa anthu 6 omwe ali pa nambala 2. Omwe simunalandire, titumizireni nambala yanu ya Airtel Money (Malawi) kapena ya TNM Mpamba ku Owinna pa Facebook kapena WhatsApp/SMS +265 880 768 511.
Kuonjezera pa ma K10,000 amene amagawana omwe aposa onse polosera bwino magemu ambiri, otsatira awo pa nambala 2 adzilandira theka la ndalama zomwe alandira apa nambala 1 kapena adzigawana K10,000 kuti pamodzi mphoto ya pa nambala 2 isadutse yomwe onse apa nambala 1 alandira.
Yambani kulosera magemu ambiri pa Owinna.com kuti nanunso zisakuphonyeni ndalamazi.
@inasio.mateyu Takutumizirani ndalama yomwe mwawina π
Fcb nyasa big bullets tiyiyamikela pa tchito angwila lelo tinakaluz km mulungu wakana
MARINICA WAYAMIKIRA MABEDI
Mphunzitsi wakale watimu yampira wamiyendo ya dziko lino Marian Mario Marinica wayamikira Patrick Mabedi kamba kochita bwino ndi timu ya Flames kumpikisano wa Cosafa wachaka chino omwe ukuchitikira ku Durban dziko la South Africa.
Malawi yalephera kufika ndime yotsiriza ya mpikisanowu dzulo pomwe yafa 3-0 kudzera pa mapenalty mumphindi 90 masewero anathera 1-1 koma inapambana masewero onse a mugulu kuti ifike mu ndimeyi.
Marinica wati Mabedi ndi mphunzitsi wabwino kwambiri ndi chifukwa chake iye anamutenga kuti akhale omuthandizira pa nthawi yake kutimuyi.
"Ndiyamikire Mabedi komanso anyamata pantchito yotamandika yomwe agwira kumpikisano wachaka chino, Palibe yemwe amapereka mpata kuti angachite motere. Mabedi ndimphunzitsi odziwa pantchito yache ndiye chifukwa munthawi yomwe ndinali mphunzitsi wa Malawi ndinamukhulupilira kuti akhale wachiwiri wanga," watero Marinica kuuza Garry Chirwa wa Nation Newspaper.
Malawi ikumana ndi South Africa loweruka
MAPOINTSI ATATU KUTI CHITIPA IFIKE PAMWAMBA
Timu ya Chitipa United ikusiyana ma pointsi atatu okha ndi omwe akutsogolera ligi ya TNM, FCB Nyasa Big Bullets pomwe anachita kuchokera kumbuyo kuti agonjetse Mighty Wakawaka Tigers 2-1 pa bwalo la Karonga loweruka.
Stimella Muyira anamwetsa pa penate pa mphindi 74 kuti abwenze Chigoli cha Zikani Munthali cha mchigawo choyamba ndipo Rajab Nyirenda anamwetsa chigoli chopambanira pa mphindi 85 kuti asunge malo a pachitatu mwa mphamvu.
Mphunzitsi watimuyi, MacDonald Mtetemera anali okondwa atapambana masewerowa ponena kuti apambana mmasewero ovuta kwambiri.
"Chiyambireni ndine okondwa chifukwa tapambana masewero ovuta kwambiri, ndimadziwa kuti Tigers indizunguza poti imandidziwa kunja ndi mkati koma tithokoze Mulungu anatipatsa nzeru mchigawo chachiwiri kuti tipeze chipambano." Anatero Mtetemera.
Kutsatira kupambana kumeneko, Chitipa ili ndi mapointsi 23 pomwe yasewera masewero 13 ndipo ikutsalira ndi atatu okha kuti ipeze Bullets.
"NDAIKA ZIGOLI 20 KUTI NDIGOLETSE" - NYONDO
Katswiri wa timu ya Dedza Dynamos, Clement Nyondo, wati ndi okondwa ndi mmene akuchitira mu ligi ya TNM pomwe iye akutsogola ndi zigoli mu ligiyi.
Nyondo anagoletsa chigoli chake chachikhumi mu ligiyi pomwe timu yake ya Dedza yalepherana 2-2 ndi FCB Nyasa Big Bullets loweruka latha. Iye wati anali okondwa kugoletsa ndi Bullets pomwe akuti Bullets imazimva kuti amatha mpira.
"Ndithokoze Mulungu pondipatsanso chigolichi komanso kuti ndawaposa anthu ena, linali khumbo langa kugoletsa ndi Bullets poti amazimva kuti amatha mpira kwambiri." Iye anatero.
Nyondo, yemwenso amatchedwa kuti ndi Cristiano Ronaldo, wati akufuna chaka chino atagoletsa zigoli makumi awiri kuti akhale omwetsa zigoli zambiri. Pa zigoli 16 zomwe timu yake yamwetsa, 10 ndi zake.
"BULLETS IMAYENERA KUGONJA" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati ndi okondwa ndi mmene anyamata ake anasewerera mmasewero awo ndi Dedza Dynamos pomwe wati kufanana mphamvu ndi timuyi ndi mwayi poti amayenera kugonja.
Munthali amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi inachokera kumbuyo kawiri kuti alepherane 2-2 ndi Dedza Dynamos mmasewero omwe anaseweredwa pa bwalo la Kamuzu. Iye anati Bullets sinali bwino ndipo ikagonja mmasewerowa.
"Ndingowathokoza anyamata poti anabwera mmasewerowa ndikufananitsa mphamvu, masewero anativuta, Dedza inatipatsa ntchito yambiri ndipo timayenera kugonja koma anyamata anazipereka, kufanana mphamvu ndi kwabwino kwa ife." Iye anatero.
MacFarlane Mgwira ndi Hassan Kajoke anagoletsa zigoli ziwiri zomwe amabwenza pa zigoli za Clement Nyondo ndi Limbani Phiri kuti alepherane pa bwaloli. Bullets tsopano ili ndi mapointsi 26 pa masewero 13 mu ligi ya TNM.
NYONDO HAS 63% OF DEDZA DYNAMOS' GOALS
Dedza Dynamos' forward, Clement Nyondo, continues to the team's big hub after scoring 10 of the team's 16 goals this season to top the scoring chart in the TNM Super League.
Nyondo got his 10th goal with an opener against FCB Nyasa Big Bullets on Saturday as the team claim an away point in a 2-2 draw at the Kamuzu Stadium.
He is now two goals ahead of Lanjesi Nkhoma of Nyasa Big Bullets as he is eyeing his first golden boot award if he continues his sparkling form this season.
62.5 - Nyondo has scored 62.5 percent of the goals scored by Dedza Dynamos this season.
The forward is in his second season with the team after joining them from Karonga United last year.
Nyerere zenizeni za mighty wanderers
BLUE EAGLES YAIMITSA KUWALI
Timu ya Blue Eagles yaimitsa mtsogoleri wa osewera atimuyi, Schumacher Kuwali, kuti asatengepo mbali pa masewero atimuyi kuyambira pano kupita mtsogolo pomwe timuyi yamupeza olakwa popanda ulemu.
Mu kalata yomwe timuyi yatulutsa lachisanu yati katswiriyu anasowa khalidwe pomwe amayankhula mosakhala bwino kwa osewera anzake ndi akuluakulu ena ophunzitsa timuyi.
Timuyi yati katswiriyu asiya ikuoneka kutimuyi kuyambira tsopano ndipo nthawi yodzabwereranso sikudziwika poti adzachita kumuuza.
Masewero oyamba iye osapezekapo ndi omwe timuyi ikusewera ndi Karonga United pa bwalo la Nankhaka lamulungu likudzali.
NYASULU IN A DAY TO REMEMBER
Flames goalkeeper, Innocent Nyasulu, had a mixed a day on Friday after making his first appearance in Red colours as he was trusted to make saves in the penalty shootout but saved none as the Flames lost 3-0 to Lesotho.
Nyasulu was introduced on 86th minute for first choice, Brighton Munthali as the game was tied on 1-1 when the coach was planning for penalty shootouts.
Nyasulu went to wrong directions in two kicks but could not save the final one from the opponent's goalkeeper, who saved three penalties for his team.
This was the first minutes for Nyasulu who has been trusted to be Flames' second Choice by Patrick Mabedi but his introduction has been criticized by People in Malawi.
MABEDI CONGRATULATES PLAYERS DESPITE LOSS
Malawi National team head coach, Patrick Mabedi had congratulated his charges after a brilliant showing at the COSAFA Cup despite the team's failure to reach into the final.
Flames lost 3-0 on penalties to Lesotho after a 1-1 draw in the 90 minutes despite having a numerical advantage as Lesotho played with a man less due to a red card.
After the game, Mabedi said his players failed to use their chances in the match but their display was very good.
"I have to give credit to my players. They did their best and we struggled to penetrate Lesotho defence as they dug deep. We had opportunities too but we missed them. We were not composed enough. Sometimes you need to be patient and not be rushing. But all in all we did all we could. It just wasn't our day." Said Mabedi.
The team will play South Africa on Saturday in the tournament's third place match.
"SULOM YANGOMUDA DE JONGH" - SILVER
Timu ya Silver Strikers yalemba kalata ya masamba asanu ndi imodzi (6) ku bungwe la Super league of Malawi kuti lichotse milandu yomwe yaikidwa kwa mphunzitsi wawo, Peter De Jongh kamba koti zaonetsa kumuda, kumuipitsira mbiri, kumusala, kusayendetsa bwino komanso kukondera kwa anthu ena.
Mukalatayi, timuyi yati SULOM sinafunse okhudzidwa pa nkhaniyi monga omwe amayang'anira masewerowa, oyimbira, apolisi, achitetezo ndi ena komanso sanapereke kalata iliyonse kutimuyi maola 72 asanakayankhe milanduyi monga mwa lamulo.
Iyo yati De Jongh anangothamanga mu bwalo la zamasewero pomwe ena sanafunsidwepo ngati matimu a Wanderers ndi Tigers anamenyanako, Bullets inalowa cha futa mmbuyo ndi bus komanso mmabwalo ena.
Timuyi yati mmene bungwe la SULOM likugwirira ntchito, ndi zosiyana ndi mfundo zomwe mtsogoleri wa bungweli, Fleetwood Haiya, ananena kuti asintha kumpira waku Malawi.
0996666212
MBC IWONETSA MASEWERO A MALAWI
Kanema wa dziko la Malawi, Malawi Broadcasting Corporation (MBC) walengeza kuti awonetsa masewero apakati pa Malawi ndi Lesotho omwe ndi ndime yamatimu anayi kumpikisano wa COSAFA mdziko la South Africa.
Mmodzi mwa akuluakulu a kanemayi, Chisomo Mwamadi, wati iwo apeza chilolezo choulutsa masewerowa pa MBC Tv, MBC 2 On the Go komanso Radio 2. Iye watinso ngati timuyi ifike ndime yotsiriza, iwo adzaonetsanso.
"Timu ya Flames yachita bwino kwambiri kumpikisanoeu, nde tinayesetsa ngati MBC kuti Mmalawi aliyense chimwemwechi chisamuphonye ndipo ndife okondwa kuti awonera pa MBC. Ngati Malawi ifike mu ndime yotsiriza ndekuti lamulungu adzawoneranso." Anatero Mwamadi.
Iye wati uwu ndi mwayi kuti makampani akatsatse malonda awo. Malawi ndi Lesotho onse anatsogolera gulu B ndi C aliyense kuti afike mu ndimeyi.
MALAWI COULD START DREAMING FOR THE WORLD CUP
Malawi National Football team, Flames, have been placed in what it looks like a fair group in the 2026 World Cup Qualifiers in a draw that has been conducted by Confederations of African Football on Thursday evening.
Malawi has been paired with Tunisia as top seeded team in Group H while Equatorial Guinea, Namibia, Liberia and Sao Tome and Principe are other teams in the group.
One of the Sports analysts in the country, Justin Mitambo, says this is just fair for Malawi and they can surely qualify for the World tournament.
"Surely, the draw had favoured us, we only have Tunisia as a tough opponent but with the confident the team has now after performing well at the COSAFA Cup, we can stop them. The other teams are average ones while the likes of SΓ£o Tome are our samousa." Said Mitambo.
In the latest changes of the qualifications, the winners of each groups will go straight to the World Cup. Malawi has never been at the tournament.
Maravihossa ππ²πΌ
2026 FIFA WORLD CUP - AFRICA QUALIFIERS DRAW
The draw for the 2026 Fifa World Cup qualifiers will be held tonight (18:00) in Cairo, Egypt.
There will be nine groups with six teams each, with the group winners qualifying directly to the World Cup.
OSEWERA A FLAMES AKUCHITA BWINO KU COSAFA
Timu ya Malawi yasonkha asanu pa osewera khumi ndi mmodzi omwe bungwe la Confederations of Southern Africa Football Associations (COSAFA) lasankha kuti asewera bwino mu ndime ya mmagulu ku mpikisanowu.
Timu ya Flames ndi yokhayo yomwe yapambana masewero onse atatu komanso osagoletsetsa chigoli chilichonse ndipo osewera awo anachita bwino mmasewero awo.
Goloboyi, Brighton Munthali, otseka kumbuyo Dennis Chembezi ndi Alick Lungu komanso omwetsa zigoli Lanjesi Nkhoma ndi Chawanangwa Kaonga ndi omwe asankhidwa mutimuyi.
Kuchita bwino kwa timuyi kwapangitsa kufika mu ndime yamatimu anayi kumpikisanowu pomwe akumane ndi timu ya dziko la Lesotho lachisanu likudzali.
This is the 2026 World Cup Qualifiers draw in 9 groups of 6 teams each.
The winners of each group will qualify straight to the World tournament in USA.
WALTER WAPAMWAMBA KU CAF
Mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi, Walter Nyamilandu Manda, wapambana pa chisankho chaku Confederations of African Football ngati mmodzi wamu komiti yaikulu ya bungweli oyimira kummwera kwa Africa.
Nyamilandu wapambana chisankhochi ndi mavoti 36 kuposa waku Mauritius, Mohammed Ally Samir Sobha yemwe anapeza mavoti 15 komanso waku Lesotho Mokhosi Philip Mahapi yemwe anapeza mavoti anayi (4).
Nyamilandu akhala pa mpando umenewu mpaka mu chaka cha 2027. Iye wagwiraponso ngati mmodzi mwa akuluakulu a khonsolo ya FIFA mmbuyomu.
CHIWAULA WAPEREKA JERSEY KU CIVO
Mlembi wamkulu wakale kutimu ya Civo United, Ronald Chiwaula, wapereka ma jersey atsopano kutimu ya Civo lachinayi ku nyumba ya timuyi.
Chiwaula wati iye wachita izi kuti timuyi izimukumbukira poti kudziwa ntchito kwa iyeyu anayambira ku timuyi. Iye wati anawona chosowa chifukwa chake anabwerapo ndi kuthandiza.
"Ndisanapite ku SULOM ndinachokera kuno nde ndinaona kuti masewero 12 kapena 13 omwe asewera agwiritsa ntchito Jersey imodzi nde iyiyi iwathandiza kuti azisinthira. Ndikufuna adzindikumbukira ndi chifukwa chake pa mkono palembedwa dzina lomwe anandipatsa kutimuku loti Lonto." Iye anatero.
Chiwaula wati ndi wokonzeka kuthandiza timuyi ngati itamufikira koma zizitengera ngati iye azikwanitsa kutero. Iye anachoka kutimuyi pomwe anapeza mpando ku bungwe la Super League of Malawi chaka chino.
NYAMILANDU ATHA KUPEZA MPANDO KU CAF
Mtsogoleri wa timu ya Football Association of Malawi, Walter Nyamilandu Manda, akhonza kupeza mpando mu komiti yaikulu ku bungwe la Confederations of African Football pomwe akupikisana ndi anzake awiri pa chisankho cha lero.
Nyamilandu akupikisana ndi mtsogoleri wa bungwe loyendetsa masewero ku Lesotho, Mokhosi Philip Mahapi komanso waku Mauritius, Mohammed Ally Samir Sobha pa woyimilira mabungwe akummwera kwa Africa kuno.
Zisankhozi zichitika lero pomwe kuli mkumano waukulu ku bungwe la CAF ndipo akhalenso akusankha atsogoleri a mmakomiti osiyanasiyana ku Abidjan mdziko la Cote d'Ivoire.
Iye anakhalaponso mmodzi wamu khonsolo la FIFA mu zaka za mmbuyomu ndipo akhonza kupezanso mpando waku FAM kachisanu mmwezi wa December mu chisankho cha FAM.
"MABEDI NDI KATUNDU" - NYAMILANDU
Mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi, Walter MacMillan Nyamilandu Manda, wayamikira mphunzitsi wogwirizira watimu ya Flames, Patrick Mabedi poitsogolera kuti timuyi ichite bwino ku mpikisano wa COSAFA wa chaka chino.
Nyamilandu amayankhula izi pomwe timuyi yangotsala ndi masewero awiri okha kuti apambane chikhochi koyamba mu mbiri ya mpira ndipo yagonjetsa matimu onse omwe akumana nawo.
Iye wati Mabedi wabweretsa kusintha kwakukulu kutimuyi ndipo wayamikira aphunzitsi ndi osewera polimbikira.
"Aphunzitsi onse otsogozedwa ndi Mabedi komanso osewera achita bwino kwambiri ndipo abweretsa Chimwemwe kwa ife. Chifukwa choti tinasintha aphunzitsi, kaseweredwe Kasintha ndipo abweretsa katsopano komwe osewera akukatha." Anatero Walter.
Mabedi analowa mmalo mwa Mario Marian Marinica yemwe waphunzitsa timuyi kuchokera mu 2022 koma zipatso sizimaoneka. Iye wapambanako masewero atatu ndi kufanana mphamvu kawiri pa masewero asanu ake kutimuyi.
"SIZOPHWEKA KUGONJETSA WALTER NYAMILANDU" - MWENDA
Wachiwiri kwa mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi wakale, James Mwenda, wati si ntchito yophweka kugonjetsa Walter Nyamilandu Manda pa mpando wautsogoleri wa FAM pomwe waonetsa chidwi choimanso pa chisankho cha bungweli mu December.
Mwenda anaimapo pa mpandowu mu 2019 atagwira ngati wachiwiri kwa Nyamilandu kuchokera 2014. Iye wati ali ndi chidwi chodzaima nawo pa mpandowu.
"Ngati anthu omwe amavota ku FAM atandipatse mpata ondisankha, sindidzaganiza kawiri ndipo ndidzaimira." Anatero Mwenda.
Iye anati anamva kuwawa atagonja pa zisankho za mpandowu koma wakonza molakwika monse ngakhale akudziwa kuti akukumana ndi namandwa pa nkhani zamasewero.
"Ndikudziwa ndikukakumana ndi nkhalakale pa nkhani zamasewero, sizophweka kuti umupambane ndipo zikufunika masamu ndi kukonzekera kwapamwamba." Anaonjezera Mwenda.
Iwo adzapikisana ndi Nyamilandu yemwe wakhala pa mpandowu kuchokera mu 2004 mpaka pano.
REPORTS: COPPER QUEENS SEXUALLY ABUSED BY COACH
A report from South African outlet, kick off, has it that Zambia Women Football team head Coach, Bruce Mwape, has been abusing the team's players sexually and threatening them to remain silent or face punishments.
One of the players of the team, name withheld, said he forces the players to sleep with them.
"If he tells you to have sex with him, you have to say yes. It is normal in our camp to have sex with Mwape." Said the Source.
It is reported that the players have ever tipped Football Association of Zambia about the issue but they don't tackle the issues because of the performance of the team.
"Maybe they turn out the allegations because it looks good to the public with results but inside it is ugly." Said another player.
Meanwhile, FAZ is reportedly to have received the issues in August last year but have not done anything. It says the issue have been taken to FIFA and Police as they do not have official complaints.
KAIZER CHIEFS IKUFUNA LANJESI NKHOMA
Tsamba lolemba nkhani zamasewero mdziko la South Africa, Soccer Laduma, lati timu ya Kaizer Chiefs ikufuna katswiri wa timu ya Flames, Lanjesi Nkhoma, kuti akatumikire timuyi.
Tsambali lati mmodzi mwa anthu omwe ali pafupi ndi osewerayu wawauza kuti Chiefs yaonetsa chidwicho kamba koti katswiriyu wachita bwino ndi timu ya Flames komanso FCB Nyasa Big Bullets.
Mphunzitsi watimu ya Flames, Patrick Mabedi anakana kuikapo mlomo kwambiri koma wati ali ndi osewera ambiri abwino mu timu yake ndipo nzosadabwitsa kuti matimu afuna osewera ambiri.
Nkhoma wagoletsa chigoli chimodzi ku mpikisanowu pomwe anamwetsa ndi timu ya Seychelles lamulungu ndipo ali ndi zigoli 8 mu ligi ya TNM ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets.
Oooooo
Next fixture
Next fixtures added
WAPOLISI ANAKWENYEDWA NDI OYIMBIRA
Malipoti akusonyeza kuti oyimbira pa masewero a pakati pa FCB Nyasa Big Bullets ndi Blue Eagles, Mayamiko Kanjere anakwenya osewera wa timu ya Blue Eagles, Micium Mhone, osewerayu atamuputa posamuyankhula mawu abwino.
Izi zadza pomwe wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Christopher Sibale anadandaula kuti timu yake inagonja masewero chifukwa oyimbira anaopseza osewera atimuyi. Koma limodzi mwa masamba olemba nkhani dziko muno, Wa ganyu, linafuna kufunsa Kanjere koma anakana kuyankhulapo.
Koma mmodzi mwa omwe amapereka chitetezo pamasewerowa anauza tsambali kuti Mhone ndiyemwe anayambitsa.
βMicium adalankhula mawu amene sadasangalatse Kanjere ndipo iye anati kuopsezedwa sikumagwira kwa iye. Adati ine ndekha ndimamenya ndiye iyiyi ndi ya iweyo ndi ineyo tithane. Adati iyiyi siyopatsananso makadi koma iwe ndi ine nde Mu tunnel mujatu ndiye ref adamukwenya Micium mpaka tidaleretsa.β Iye anatero.
DE JONGH AKAYANKHA MLANDU LERO
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter De Jongh, akuyembekezeka kukakumana ndi komiti yokhazikitsa bata ku bungwe la Super League of Malawi lero pomwe akayankhepo pa milandu ofuna kuyambitsa ziwawa mmasewero a mpira wamiyendo.
Mphunzitsiyu anathamangira kuti akamugwiregwire oyimbira pomwe timu yake inalepherana 0-0 ndi Chitipa United pa bwalo la Civo masabata awiri apitawo ndipo anthu ena anachita kumugwira iye.
Iye walandirako kalata yofiira imodzi ndi achikasu atatu pa miyezi inayi yomwe wakhala ku Malawi kuno kamba kosaonetsa khalidwe labwino. Mkumanowu uchitikira ku hotel ya Lilongwe lero.
Malawi vs comoros
KARONGA UTD'S DEDICATES WIN TO HIS LATE MOTHER
Karonga United's captain, Eric Atsigah, dedicated his team's cone back win against Dedza Dynamos on Sunday to his late mother who died last month but was buried last Saturday.
The Ghanaian international lost his mother in June after a long illness and was raid to rest last Saturday ahead of Karonga's match.
In the game, Saulos Moyo and Josiah Duwa netted goals to eclipse Clement Nyondo's goal to claim a 2-1 win and after the game, Atsigah wore a vest written 'RIP MUM'.
The former Wanderers player then posted on his Facebook account that the three points belong to his mother. The win took the team out of the relegation zone to 13th on the table with 14 points.
BREAKING: FIFA RIFTS ZIMBABWE'S BAN
Football is set to return normally in one of the nearest countries of Malawi, Zimbabwe, after FIFA has lifted the suspension posed on Zimbabwe Football Federation (ZIFA) on 24th February 2022.
This development comes after ZIFA met what they were told to do among them, thats, the repeal of sports and recreation committee (SRC) of 26th November 2020 suspending the ZIFA general Secretary, as per communication from the Worlds governing body.
FIFA banned Zimbabwe from participating in all international competitions due to the government interference in the running of the Association and The country's federation was suspended by the sports and recreation commission hence the commission were supposed to reinstate the suspended Felton Kamambo- led ZIFA board if it wanted the suspension to be lifted.
Meanwhile, their national team will start again getting involved in different competitions while their clubs will now return in CAF tournaments.
1-1
"OYIMBIRA ANATIOPSEZERA OSEWERA" - SIBALE
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Blue Eagles, Christopher Sibale, wati timu yake sinasewere bwino mu chigawo chachiwiri cha masewero awo ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets kamba koti oyimbira anaopseza kuti osewera atimuyi amenyedwa.
Sibale amayankhula izi atatha masewerowa kwa atolankhani ndipo anati timu yake ikanatha kuchita bwino koma oyimbira anawachotsa kulimbikira kwa osewera.
"Tinasewera bwino mu chigawo choyamba pomwe tinapeza mipata yochuluka koma titasintha, oyimbira anawauza osewera athu koma osewera mmodzi amenyedwa ati poti timu yathu ikumamenya oyimbira." Anatero Sibale.
Timuyi ili ndi mlandu oti iyankhe pomwe sabata yatha anafuna kumenya oyimbira kamba kosakondwa ndi ziganizo za oyimbira. Mmasewero ndi Bullets, Yamikani Fodya, Hassan Kajoke ndi Ephraim Kondowe anagoletsa zigoli aliyense kuti Bullets ipambane 3-0 pa bwalo la Kamuzu.
ZIKHULUPILIRO MU MPIRA ZAVUTA KU MALAWI
Zikhulupiliro zafikapo mu masewero a mpira wamiyendo ku Malawi pomwe sabata yathayi zinaliponso mu ligi ya TNM makamaka pa bwalo la Karonga.
Loweruka, timu ya Kamuzu Barracks, inathira mkodzo pa golo la timu ya Chitipa United ati poganizira kuti eni khomowa anali ndi mankhwala omwe amakanikitsa timuyi kugoletsa.
Ndipo lamulungu, mmodzi mwa akuluakulu a timu ya Dedza Dynamos anapezeka ndi chinthu chomwe akuganizira kuti ndi chithumwa pomwe timuyi inagonja 2-1 ndi Karonga United.
Mu ligi ya chaka chino, zikhulupiliro zikuchitika kwambiri koma palibe timu Ina iliyonse yomwe yalandirako zilango za mchitidwewu.
KONDOWE WAKANA KUYANKHULA ATAGOLETSA CHIGOLI CHOYAMBA KU BULLETS
Katswiri wa timu FCB Nyasa Big Bullets, Ephraim Kondowe, wakana kuyankhulapo mmene akumvera pomwe wagoletsa chigoli chake choyamba kutimu ya FCB Nyasa Big Bullets pomwe wati pakamwa patha kumusokoneza.
Kondowe anagoletsa chigoli chake choyamba chipitireni ku timuyi pomwe anamenya bomba atangosinthana ndi Antony Mfune pa mphindi 77 mmasewero omwe Bullets inagonjetsa Blue Eagles 3-0.
Mtolankhani wa Owinna, Hastings Kasonga, anafikira Kondowe kuti ayankhulepo pa chigolichi koma iye anati kuyankhulapo zikhoza kumupatsa phuma chifukwa akhonza kulonjeza zinthu zambiri komanso zovuta.
Iye wati adzayankhulapo kutsogoloku koma pakadali pano apitilizebe kukweza mutu kuti apangebe zambiri. Kondowe anapita kutimuyi kumayambiliro a chaka chino atachotsedwa kutimu ya Mighty Mukuru Wanderers chaka Chatha.
KUMWEMBE WAYAMBAPO
Katswiri wa Flames, Christopher Jacammah Kumwembe, wagoletsa chigoli chake choyamba pomwe dzulo wathandiza timuyi kupambana 2-0 ndi timu ya Seychelles ku mpikisano wa COSAFA ku South Africa.
Kumwembe anagoletsa chigoli chachiwiri mmasewerowa pomwe anamalizitsa mpira omwe Lanjesi Nkhoma anaumenya ndipo goloboyi wa Seychelles anauchotsa.
Awa anali masewero ake achitatu ndi timuyi pomwe anasewera masewero oyamba ndi Lesotho mmasewero aubale omwe anathera 1-1 ndipo anaseweranso mphindi makumi asanu ndi imodzi mmasewero oyamba ku mpikisanowu ndi Zambia.
Mmasewero a Seychelles, iye anasewera mphindi zonse koyamba ku timuyi. Chigoli china cha Flames anagoletsa ndi Lanjesi Nkhoma. Iye analinso ndi zigoli 7 mu ligi ya TNM ku Malawi.
NYONDO WATSOGOLA NDI ZIGOLI
Katswiri wa timu ya Dedza Dynamos, Clement Nyondo, tsopano akutsogola pa ndandanda wa osewera omwe agoletsa zigoli zambiri mu ligi ya TNM pomwe ali ndi zigoli zisanu ndi zinayi (9) mu ligiyi.
Nyondo anagoletsa chigoli choonjezera pa masewero omwe timu yake inagonja 2-1 ndi timu yake yakale ya Karonga United pa bwalo la Karonga lamulungu.
Iye tsopano akutsogola pomwe Lanjesi Nkhoma ali ndi zigoli 8 pambuyo Pake komanso Christopher Kumwembe ndi Stain Davie ali ndi zisanu ndi ziwiri (7) aliyense.
1_0
Anasiya pano Ali ku zodiac ndiye tapangani so update your information