MPINGANJIRA WADYETSA BWINO MANOMA
Mtsogoleri wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Dr Thomson Mpinganjira, wayamikira anyamata atimuyi ndi ndalama zankhaninkhani pomwe timuyi yagonjetsa Silver Strikers 1-0 pa bwalo la Kamuzu lachinayi lapitali.
Mpinganjira wapereka ndalama yokwana K100,000 kwa osewera omwe anasewera nawo dzulo pomwe omwe anali panja apatsidwa ma K500,000 ndipo wati ndi okondwa ndi mmene timuyi inasewerera.
"Ndine okondwa ndi mmene timuyi inasewerera mmasewerowa ndipo ndikukhulupilira kuti apitilizabe." Mpinganjira anafotokoza.
Mtsogoleri wa osewera kutimuyi, Stanley Sanudi, anayamikira a Mpinganjira ndipo wati izi ziwathandiza kuti alimbikire.
Timuyi ili pa nambala yachinayi pomwe yatolera mapointsi 22 pa masewero 12 omwe yasewera mu ligi ya chaka chino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores