BALIKINHO ATHA KUONEKA LERO NDI SILVER
Katswiri wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Balikinho Mwakanyongo, akhonza kuonekanso kutimuyi mmasewero awo ndi Silver Strikers lachinayi pomwe mphunzitsi watimu, Mark Harrison, watsimikiza kuti wakhala akupanga zokonzekera ndi timuyi.
Katswiriyu anachoka kutimuyi chaka Chatha pomwe ananamizira kuti anali ku maliro ndipo maumboni anafika oti akusewera mdziko la Tanzania. Chaka chino, katswiriyu anafika mdziko muno ndipo kwamasabata angapo sanaoneke koma tsopano atha kuoneka ndi Silver Strikers.
Harrison watsimikiza kuti osewerayu wakhala akuonedwa ndi timuyi ndipo tsopano akhonza kuonedwa mmasewero a Silver Strikers. Iye watsimikizanso kuti Adeleke Kolawole ali kutimuyi ndipo sapezeka komanso Mphatso Kamanga ndi ovulalanso.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores