MUNTHALI WASAINA MGWIRIZANO WINA KU BLUE EAGLES
Goloboyi wa timu ya Blue Eagles, Brighton Munthali, wasaina mgwirizano womwe umufikitse mpaka chaka cha 2025 ndi timu ya Blue Eagles pomwe mgwirizano wake ukhale kumapeto a chaka chino lachisanu.
Wachiwiri kwa mlembi watimuyi, Gift Likoswe, watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati katswiriyu wakhala ofunikira kutimuyi zomwe zachititsa kuti amuonjezere mgwirizanowu. Iye wati mgwirizanowu sukusokoneza ulendo wake opita ku Black Leopards yaku South Africa.
"Mgwirizano wake umatha mu December 2023 nde taonjezera mgwirizanowu kuti udzathe mu 2025 koma sizikukhudza pa ulendo wake kutimuyi ya Black Leopards. Mukudziwa kale kuti goloboyiyu ndi nambala 1 mdziko muno ndipo tikufuna luso lake akaonetsere kunja." Likoswe anafotokozapo.
Iye anatinso mgwirizano wawo ndi Black Leopards ndi oyambira mmwezi wa July chaka chino mpaka July 2024 ndipo osewerayu akhale akupita kutimuyo.
Katswiriyu anapita kutimuyi chaka chatha kutsatira kusiyana ndi Silver.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores