CHILANGO CHOSASEWERA ZAKA ZIWIRI ATAMENYA OYIMBIRA
Timu yamu ligi yakumpoto ya SIMSO-Innobuild Northern region Football league, Chintheche United yapatsidwa chilango chosasewera masewero kwa zaka ziwiri mu mipikisano iliyonse kamba komugwira nthupi oyimbira.
Timuyi inachita izi mmasewero omwe ankasewera ndi Nkhatabay Select sabata yathayi ndipo anagonja 3-1 pomwe yasamutsidwa pa nambala yachiwiri mu gulu lawo.
Bungwe la NRFA ndilomwe lapereka chilangochi ndi cholinga chofuna kuthetsa mchitidwewu mu ligiyi.
Timuyi inali mu gulu B la ligiyi ndipo inali la nambala yachitatu ndi ma pointsi 11 atasewera masewero 9 mu gulu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores