MLANDU WA WANDERERS ULIKO PA 31 JULY
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers Football Club ikuyembeza kukayankha mlandu kwa osewera awo awiri akale pa 31 July 2023 ku bwalo la zamilandu loona za ntchito ku Blantyre.
Osewera awiriwa, Francis Mulimbika ndi Bongani Kaipa akufuna timuyi iwapatse ndalama zapafupifupi K44,280,000 kamba kothetsa migwirizano yawo mosasathata malamulo.
Mulimbika akufuna K20,902,000 ndipo Kaipa akufuna K23,378,000 kuchokera ku timuyi. Iwo anachotsedwa kutimuyi kumayambiliro a chaka chino pomwe mphunzitsi, Mark Harrison anayendetsa tsache.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores