OSEWERA AWIRI AKU FLAMES SAPEZEKA NDI MANOMA
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers sikhala ndi osewera ake awiri omwe ali ndi Flames ku South Africa komwe amasewera nayo mu mpikisano wa COSAFA Cup, Stanley Sanudi ndi Gaddie Chirwa kamba ka makalata achikasu komanso kuvulala.
Timuyi inalephera kusewera masewero awo mmasabata awiri kamba kotumiza osewera anayi ku Flames ndipo sabata ino ikumana ndi Silver Strikers komanso Blue Eagles koma popanda awiriwa.
Gaddie Chirwa anavulala mmasewero a Flames ndi Lesotho ndipo watitsimikizira kuti akumvabe ululu pomwe sanapezeke mmasewero ndi South Africa pomwe Sanudi ali ndi makalata achikasu atatu.
Winanso yemwe sapezeka ndi Silver Strikers ndi Isaac Kaliati yemwe ali ndi makalata achikasu atatunso. Kupambana mmasewero awiri atimuyi kuitengera pa ma pointsi 25 pambuyo pa Silver ndi FCB Nyasa Big Bullets.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores