"MULEMBENI MABEDI" - APHUNZITSI AKU MALAWI
Mtsogoleri wa bungwe la aphunzitsi ampira wamiyendo mdziko muno, Davie Mpima, wati bungwe la Football Association of Malawi limulembe ntchito mphunzitsi watimu dziko lino, Patrick Mabedi kamba kochita bwino mu masewero omwe watsogolera timuyi.
Mpima wayankhula izi kutsatira timuyi kumaliza pa nambala yachinayi ku mpikisano wa COSAFA Cup pomwe sanagonjeko masewero aliwonse mu mphindi 90 za masewero. Mpima wati Mabedi akuyenera kulembedweratu osati kukhalabe ogwirizira.
"Mabedi waonetsa kuti akhonza kusintha zinthu ndi osewera a mdziko momwe muno ndipo tikhonza kuchita bwino, akungoyenera kuti amulembe ntchito." Iye anatero
Mgwirizano wa Mabedi ndi bungwe la Football Association of Malawi udzatha mu mwezi wa September pomwe anatenga ntchitoyi mogwirizira kulowa mmalo mwa Mario Marian Marinica.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores