MALOYA WAPITA KU MOZAMBIQUE
Katswiri wakale wa Mighty Mukuru Wanderers, Aubrey Maloya, wasaina mgwirizano wa chaka chimodzi nditimu ya Club Ferroviario de Quelimane yamdziko la Mozambique.
Aubrey maloya anafika mdziko muno pa 15 April ndipo wakhala kwa miyezi itatu kufikila lachiwiri sabata yatha pomwe wanyamuka kubwerera mdziko la Mozambique.
Maloya anabwerera kumudzi kamba koti timu yomwe amafuna kutumikira imadikilira zitupa zolowera mdzikomo ndipo zatheka pomwe msika wogula ndi kugulitsa osewera wasegulidwa Mwezi wapitawu.
Iye anati Khumbo lake lotumikila matimu aku Malawi linalipobe ponena kuti anachotsedwa asanamalize kuchita zabwino ndi Mighty Mukuru Wanderers.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores