HAMMERS IKUFUNA NDALAMA ZAWO
Timu ya Ekwendeni Hammers imayenera kunyamuka lachinayi madzulo kulowera mu mzinda wa Blantyre komwe akuyenera kudzakumana ndi Bangwe All Stars koma alephera pomwe osewera awo anyanyala.
Malipoti aonetsa kuti anyamata atimuyi akufuna ndalama zao zomwe amalandira akapambana masewero zomwe timuyi sinawapatse kwa nthawi tsopano.
Mmodzi mwa anthu akutimuyi, yemwe sanafune kutchulidwa dzina, wati anyamatawa ananetsa kuti sanyamuka ulendowu pokhapokha apatsidwe ndalamazi.
Ekwendeni Hammers ili pa nambala yachisanu mu ligi ya TNM pomwe yatolera ma points 22 pa masewero 13 ndipo idzakumananso ndi Dedza Dynamos lolemba mu chikho cha FDH Bank.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores