"TIKANAYAMBA NDI EXTREME OSATI WANDERERS" - DE JONGH
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter De Jongh, wati akudabwa ndi bungwe la Super League of Malawi kamba kowapatsa koyamba masewero a Mighty Mukuru Wanderers osati Extreme FC angakhale kuti anayamba kuphonya a Extreme.
Mphunzitsiyu wayankhula izi patsogolo pa masewero awo ndi Manoma mu mzinda wa Blantyre pomwe wati mmene masewero aikidwira awakhaulitsa.
Iye wati masewero oyamba kusemphana nawo anali a Extreme ndipo amayenera kusewera amenewo ndipo ulendo oti apite ku Mzuzu kukakumana ndi Moyale Barracks mu chikho cha FDH Bank uwakhaulitsa poti ayenda ulendo wautali.
Timuyi yakhala masabata awiri osasewera mpira pomwe anatumiza osewera anayi ku Flames ndipo ili pa nambala yachiwiri ndi mapointsi 25 mmasewero 11.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores