Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
BULLETS IKUYANG'ANA KUTSOGOLO
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yayankhulapo pa zifukwa zomwe akusewerera masewero a mu TNM Supa ligi ngakhale ali ndi osewera anayi ku Flames komanso ena ambiri ovulala ponena kuti akuyang'ana kutsogolo kwa iwo poti akutenga nawo mbali mu mipikisano yambiri.
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu, Heston Munthali ndiyemwe anayankhula izi patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Blue Eagles lamulungu pa bwalo la Kamuzu. Iye wati iwo sakuyang'ana yamatimu ena koma iwo akupanga za Bullets basi.
"Tikumenya masewero ngati Bullets, tili ndi mipikisano yambiri yomwe tisewere nde ife tikuona kumbali yathu, enawonso adzaseweranso masewero awo koma kwa ife tikuyang'ana zomwe zili kutsogolo kwathu." Anatero Munthali.
Pa masewero awo ndi Blue Eagles, iye wati wawauza anyamata kuti akagwiritse ntchito mipata yomwe ikapezeke ndipo wati kumbali ya zigoli, ziyamba kupezeka.
"Ndikukhulupilira kuti anyamata ake ndi omwewa omwe amatipezera zigoli mmbuyomu nde zipezekanso kutsogolo
BULLETS ISEWERA CAF CHAMPIONS
Akatswiri achikho cha TNM Supa ligi, FCB Nyasa Big Bullets asewera nawo mu mpikisano wa CAF Champions league wachaka chino pomwe bungwe la Confederations of African Football lavomereza pempho lawo lotenga nawo mbali mu mpikisanowu.
Mkulu oyang'ana za club licensing ku bungwe la Football Association of Malawi, Cassper Jangale, wati Bullets inakonza zonse zoyenereza zofunika kutenga nawo mbali mu mpikisanowu ndipo wayamikira timuyi poti mpikisanowu ukuthandiza osewera kuzigulitsa mmatimu akunja.
Timuyi ili ndi mwayi wowonjezera osewera pomwe CAF ikhale ikulandira mayina omwe matimu agwiritse ntchito kuchokera pa 1 July mpaka pa 31 August ndipo mmodzi mwa akuluakulu a timuyi, Albert Chigoga wati adikira mawu a aphunzitsi kutimuyi.
"Munthu ukamapita ku nkhondo, umafunikira kutenga zida zamphamvu nde ngati aphunzitsi afune kuonjezera, ife titsatira kutero."
Bungwe la CAF yati matimu opambana ndime yachipulula yayamba azifika mmagulu kulekana ndi poyamba.
"BANGWE INATULUKA KALE MU LIGI" - MHANGO
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Nicolas Mhango, wati ndi odandaula poti timu yake yagonja ndi Bangwe All Stars yomwe akuti inatuluka kale mu ligi ngakhale yachoka ku chigwa cha matimu otuluka loweruka.
Timuyi inagoletsetsa chigoli chapa mphindi ziwiri cha Madalitso Chiume chomwe chinali chokwana kupambanitsa Bangwe All Stars pa bwalo la Mpira 1-0.
Atatha masewero, mphunzitsi wa Moyale anali okwiya ndi kayimbilidwe ndipo anati Bangwe inatuluka Kale.
"Tinasewera bwino koma ndizodandaulitsa kuti taluza ndi timu yotuluka kale, Bangwe ndinayitulutsa kale mu ligi. Red card ija simayenera chifukwa choti MacDonald Harawa ndi captain, ndi amene amayenera kumuyankhula ref koma anthu amangoti kumpoto koma izi ndaona ku Blantyre ndadziwa kuti oyimbira onse amasewera nawo." Anatero Mhango.
Kutsatira kugonjaku, Moyale ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) ndi mapointsi 16 pa masewero 12.
Malawi vs schesheles
3-0
Zampila izi
Magemu ayamba
Kusogola sikuwina league tatenga nyelele
DE JONGH AKAYANKHA MLANDU KU SULOM
Bungwe la Super league of Malawi latsegulira mlandu timu ya Silver Strikers ndi mphunzitsi wawo, Peter De Jongh kamba kofuna kumenya oyimbira sabata yatha pomwe timuyi inalepherana 1-1 ndi Chitipa United pa bwalo la Civo.
Bungweli laika tsiku la lachiwiri pa 11 July 2023 ku Lilongwe hotel kuti akamve mlanduwu pomwe ayipeza ndi mbali ziwiri zoti ayankhepo monga:
β’Kukanika kuteteza akuluakulu atimuyi ndi masapota pomwe analowa mbwalo la zamasewero.
β’Kulowetsa masewero a mpira wamiyendo kukhala zipolowe.
Akapezeka olakwa, De Jongh ndi timu ya Silver alandira chilango kuchokera ku bungweli.
Akuyenela bas kulandila chilango mwina asinthako, zomwe anachita pamenepaja sizoyenela nkukhalanso couch wa timu yaikulu ngat imeneyi
KANANJI NDI OSEWERA AKE ATSEGULIRIDWA MILANDU
Bungwe la Super league of Malawi (Sulom) latsegulira mlandu ena mwa akuluakulu komanso osewera atimu ya Blue Eagles kamba konyazitsa masewero ampira wamiyendo pomwe timuyi imasewera ndi Ekwendeni Hammers pa 2 July 2023 pabwalo la Mzuzu.
Pamasewerowa anthuwa sanakhutire ndimomwe Oyimbira Rose Zimba, Pierre Kumwenda,Khumbo Madhlopa komanso Mike Misinjo posakhutira ndimomwe anagwilira ntchito zomwe zinapangitsa kuti awathamangitse pamapeto pa masewerowo.
Anthu omwe Sulom yatchula kuti ayankhe mlandu ndimonga:
Eliya Kananji Christopher Sibale Chimwemwe Chitedze Schumacher Kuwali Micium Mhone Tonic Viyuyi Lanken Mwale Chakonda Majanga Richard Lapson
Ngati anthuwa apezeke olakwa akhale akupatsidwa chilango
Zili motan
Update chitipa is winning
resuits
2-1
CHIMANGO KAYIRA SALUTES ARNOLD
Former Flames defending midfielder, Chimango Kayira, has saluted the current defending midfielder of the team, Lloyd Arnold, after his stellar performance in his dream competitive debut with the team on Thursday as they defeated Zambia 1-0 at the COSAFA Cup.
Arnold was brilliant in the game which has made him earn praises from sports spectators in the country and Kayira says the Civo United player has a bright future.
"He executed his duties without fear The future looks bright. We hope he will grow and build confidence from such marvelous displays." Said Kayira.
Arnold made his first appearance with the Flames in a friendly against Mozambique last month and the Zambia match was his first in a recognized competition and played the whole minutes.
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yaika katswiri wawo wakale, Fischer Kondowe, kukhala wachiwiri kwa mphunzitsi watimu pomwe alowe mmalo mwa Peter Mponda.
Kondowe wakhala akugwira ntchito ngati mmodzi mwa aphunzitsi kutimuyi koma wakwera udindo kamba kochoka kwa Mponda.
Peter Mponda anachoka kutimuyi pomwe anapeza ntchito ngati wachiwiri kwa mphunzitsi kutimu ya Black Leopards ku South Africa.
KAMWENDO WABWERERA KU DEDZA
Timu ya Dedza Dynamos sikhala ndi osewera awo anayi, Charles Chipala, Alex Benson, Lameck Gamphani ndi Gift Magola omwe ali ovulala patsogolo pa masewero awo ndi Karonga United ku bwalo la Karonga.
Timuyi koma tsopano ilandiranso katswiri wawo, Promise Kamwendo, yemwe sanasewere masewero a Mighty Mukuru Wanderers, Chitipa United ndi MAFCO kamba koti anavulala koma tsopano wachira.
Katswiri yemwe ali ndi zigoli zambiri mu ligi ya TNM, Clement Nyondo, ndi yemwe watsogolera timuyi pomwe yanyamuka kulowera ku Karonga. Ndandanda wa osewera omwe ali nawo pa ulendowu uli pa chithunzichi:
"CHIZUNGU CHIKUFUNIKIRA PA ANTHU" - LIWEWE
Mmodzi mwa atolankhani a nkhani zamasewero mdziko muno, Steve Liwewe Banda, wati makono anthu akufunikira kudziwako kachingerezi pang'ono ndi cholinga choti azilumikizana ndi anthu ammayiko osiyanasiyana poti chiyankhulochi chimagwiritsidwa ntchito mmayiko ambiri.
Liwewe amayankhula izi kutsatira katswiri wa timu ya Flames, Alick Lungu, anakanika kuyankhula mu chingerezi pomwe anasewera bwino mmasewero atimuyi ndi Zambia ku COSAFA ndipo James Sangala ndiye amamutanthauzira.
Liwewe wati ndi zofunika kuti anthu adziweko ngakhale pang'ono chingerezi poti zinthu zambiri monga kufunsira ntchito, kukambirana mu nyumba ya malamulo komanso ndondomeko za mankhwala ndi zina zimakhala mchingerezi.
"Kumangofunika kudziwako chingerezi pang'ono ngakhale utaphotchola amvabe kuti ukufuna chiyani. Chosangalatsa pano nchakuti ife makolo ngakhale sukulu inativuta timayesetsa kuti ana athu aphunzire chizungu." Anatero Liwewe.
Timu bora iyo ya 0 kwa 6
Live
Mussh
992002627
Ezala ndi Judth agawana K10,000πΈ atalosera molondolaπ― magemu 10 pa Owinnaβ½ Monday - Sunday π
Nanu loserani magemu ambiri pa Owinna.com kuti muchulutse mwayi wowina ma 10 pin sabata iliyonse.
malawi 1 1 zambia prediction
Malipoti amveka kuti unifolomu ya timu ya Mighty Mukuru Wanderers yomwe amayenera kugwiritsa ntchito pa masewero a chaka chino yafika tsopano.
Izi ndi malingana ndi zomwe zikulembedwa pa masamba a mchezo.
"TIKHOZA KULANGA SULOM" - FAM YACHENJEZA
Bungwe la Football Association of Malawi lachenjeza bungwe la Super League of Malawi kuti lili ndi mphamvu zopereka zilango ku bungweli ngati angapitilize mchitidwe wosamvera komanso mwano kwa iwo.
Mu kalata yomwe yasainidwa ndi mlembi wamkulu, Alfred Gunda, yati bungweli likuchita ukamberembere wosamvera zina zomwe FAM inaika mmalamulo ake.
Iyo yati SULOM inachita zosemphana posaimitsa masewero a matimu omwe atumiza osewera odutsa atatu ku Flames pomwe akuti anasemphana ndi gawo 49 ya mmalamulo a SULOM. FAM yati SULOM ichotse masewero a matimuwa ndipo kupanda kutero, chilango chidzawatsatira.
Mabungwe awiriwa aonetsa kuchita zinthu mosagwirizana pomwe zaoneka masabata apitawa pomwe SULOM inakana kuchotsa masewero a Bullets ndi Wanderers pa bwalo la Kamuzu ndipo SULOM sinapereke ndalama za pakhomo ku FAM.
Matimu a Silver Strikers, Mighty Mukuru Wanderers komanso FCB Nyasa Big Bullets atumiza osewera anayi iliyonse ku Flames.
Bungwe la Super League of Malawi (SULOM) lasuntha masewero awiri amu TNM Supa ligi sabata ino kufikira mmasiku osadziwika pomwe matimu a Mighty Mukuru Wanderers ndi Silver Strikers atumiza osewera ochuluka ku timu ya Flames.
Bungweli lachita izi litakana koyamba kuti masewero onse amu ligi achitika mu sabata ino koma tsopano bungweli lati masewero a Mighty Mukuru Wanderers ndi MAFCO komanso Silver Strikers ndi Extreme FC sachitika kamba koti Silver ndi Noma anatumiza osewera anayi ku Flames.
Koma ngakhale FCB Nyasa Big Bullets inatumizanso nambala ya osewera omwewa, timuyi yati isewerabe masewero awo ndi Blue Eagles lamulungu likudzali.
TEMWA WAVUTA KU CHINA
Katswiri wa timu ya Scorchers, Temwa Chawinga, akuchita bwino ku ligi yaku China pomwe wagoletsa zigoli zisanu ndi ziwiri (7) kuti atsogole ndi zigoli mu ligi yaku China.
Temwa, yemwe ndi mng'ono wake wa Tabitha, yemwe anamwetsa zigoli zambiri ku Italy, anagoletsa zigoli zisanu (5) sabata yatha pomwe Wuhan Jiangda inapambana 13-0 ndi Fuoshan ndipo lolemba lapitali, anagoletsa zigoli ziwiri (2) ndi Quangxi pomwe timuyi inapambana 4-1.
Temwa tsopano wagoletsa zigoli zochuluka mu ligiyi pomwe ali ndi zigoli khumi (10).
Temwa wakhalapo katswiri omwetsa zigoli zambiri ku China chaka Chatha pomwe anathandizanso timu yake ya Wuhan Jiangda kukhala akatswiri a ligi.
EAGLES ILANGA OSEWERA OTHAMANGITSA OYIMBIRA
Timu ya Blue Eagles yati ipereka chilango kwa osewera aliyense amene anakhuzidwa ndi mpungwepungwe umene unachitika pakutha pa masewero a timuyi ndi Ekwendeni Hammers mu ligi ya TNM ku Mzuzu la mulungu lapitali.
Mlembi wamkulu wa timuyi, Benjamin Msowoya, watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati mchitidwewu wayipitsa mbiri ya nthambi yopereka chitetezo ya Police.
Iye wati akuluakulu a nthambi ya Polisi mdziko muno yati osewera omwe anathamangitsa oyimbirawa alandire chilango kamba kosowa khalidwe.
Eagles inagonja masewerowo ndi Ekwendeni Hammers 1-0 ndipo osewera anathamangitsa oyimbira mpira Rose Zimba ndi omuthandizira ake mcholinga choti awamenye ati posakhutira nawo kuti sanagwire ntchito yawo bwino. Izinso zinachititsa kuti apolisi aponye utsi wokhetsa Misonzi pa bwalo la Mzuzu.
1~1
BLUE EAGLES YATCHAYIDWA MMIMBA
Timu ya Blue Eagles yayenera kukhala modandaula pomwe osewera awo atatu, Micium Mhone komanso magoloboyi awiri odalilika, Brighton Munthali ndi John Soko sapezeka kutimuyi mpaka kumapeto kwa ligi ya chaka chino.
Timuyi yatsimikiza za nkhaniyi ndipo yati Munthali akulowera ku South Africa kutimu ya Black Leopards pa ngongole ya chaka chimodzi pomwe Mhone ndi Soko apita kumaphunziro a miyezi isanu ndi umodzi (6) ku sukulu ya apolisi ku Blantyre.
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimuyi, Christopher Sibale anati ziwakhudza kwambiri koma atenga goloboyi mmodzi kutimu yawo yachisodzera kuti akakhale limodzi ndi Chakonda Majanga yemwe anali wachitatu kutimuyi.
Ena mwa omwe atenge nawo mbali pa maphunzirowo ndi osewera akale, Stuart Mbunge, Charles Ngosi, Chimwemwe Kalanje, Steven Chagoma, Wongani Ngulube, Maxwell Salambula, Japhet Mambelera, Aubrey Mayuni ndi Dan Phiri.
Thanks for your information
SULOM SINAPEREKE NDALAMA KU FAM
Bungwe la Football Association of Malawi likufuna ndalama yokwana K4.7 million kuchokera ku Super League of Malawi pa ndalama zomwe zikapezeka pa masewero a Mighty Mukuru Wanderers ndi FCB Nyasa Big Bullets.
Bungwe la SULOM silinapereke ndalamazi ku FAM pomwe bungweli linasambira mmanja SULOM kamba koyika masewero aakulu pa bwalo la Kamuzu zomwe FAM imakana.
Atatha masewero, ndalama yokwana K56.4 million ndiyomwe inapezeka pa masewerowa ndipo K4.7 million zinapite ku FAM monga mmene zimayenerera.
Bungwe la SULOM silinayankhepo pa nkhaniyi pomwe mkulirano ukuchulukirabe.
keep it up sulom apa mwabwera
DE JONGH ALANDIRA CHILANGO
Bungwe la Super league of Malawi, ikudikira malipoti kuti iunike khalidwe lomwe mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter De Jongh anaonetsa pomwe timuyi inafanana mphamvu 0-0 ndi Chitipa United pa bwalo la Civo.
Mlembi wa bungwe la SULOM, Williams Banda wati izi ndi zochititsa manyazi ndipo khalidwe lake siloyenera kuonetsa iyeyu monga mphunzitsi.
Banda wati bungwe lawo lidikira malipoti ammasewerowa ndipo De Jongh akhonza kulandila chilango. Mmasewerowa, ochemerera wina wa Silver anakathira mkodzo pa golo la Chitipa ndipo bungweli liunikanso pa milandu.
De Jongh wakhala asakuonetsa khalidwe labwino chipitireni ku Silver Strikers ndipo anthu osiyanasiyana adzudzula mchitidwe wakewu
MANOMA
SULOM ON FAM'S NECK
The relationship between Super League of Malawi and Football Association of Malawi which has been seen in the previous weeks to be sour, is still breaking as SULOM releases TNM Super League fixtures despite the Flames involvement in the COSAFA Cup this week.
The development comes after the teams will have tough games despite providing some players at the national team which can make teams deny their players for the team.
The Flames are under FAM which means they need to sweat in order to convince teams to provide them with players for the tournament. This is how the fixture looks.
SATURDAY 8 JULY
-Chitipa United V Kamuzu Barracks @Karonga -Bangwe All Stars V Moyale Barracks @Mpira -MAFCO V Mighty Mukuru Wanderers @ Chitowe -Extreme V Silver Strikers @Civo Stadium
SUNDAY 9 JULY -FCB Nyasa Big Bullets V Blue Eagles @Kamuzu Stadium -Karonga United V Dedza Dynamos @Karonga -Civo United V Ekwendeni Hammers @ Civo
SINGINI NDI THANTHWE LA EKWENDENI
Katswiri wa Ekwendeni Hammers, Blessings Singini, akuchita bwino kwambiri pomwe wagoletsa zigoli zinayi mmasewero atatu otsogozana omwe Ekwendeni Hammers yasewera.
Singini amasewera pakati motchinga kutimuyi ndipo ntchito yogoletsa singakhale kwambiri ya iyeyu koma anagoletsa chigoli chomwe chinapambanitsa Hammers pomwe imamenya ndi Extreme FC sabata yatha.
Iye anagoletsa zigoli ziwiri pomwe ankamenya ndi Airborne Rangers mmasewero amu FDH Bank Cup ndipo sabata ino, chigoli chake chatengera timuyi pa nambala yachinayi pomwe waipambanitsa 1-0 ndi Blue Eagles.
Iye walowa mmalo mwa Mphatso Magaleta yemwe amagoletsera kwambiri timuyi koma pano iye ndiye mutu wa timuyi.
KHUDA WASIYANA NDI POLOKWANE
Bwalo lalikulu ku South Africa la Gauteng High Court lagamula kuti katswiri wa Flames, Khuda Muyaba ndi timu ya Polokwane City alekana kutsatira kuthetsa kwa mgwirizano wawo.
Muyaba watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati iye ndiyemwe anakapereka pempho ku bwaloli kamba kosemphana ndi timuyi.
"Nditha kutsimikiza ndithu kuti zatheka. Apapa ndine free agent.β iye anauza tsamba la Wa Ganyu.
Khuda wati sakubwereranso ku Malawi ndipo matimu angapo aku South Africa akumufuna katswiriyu. Ena mwa iwo ndi Royal AM ndi Black Leopards omwe amveka kuti akumufuna katswiriyu.
how many goals scored so far
1:0
Maghty tose lachinayi kukayipasa moto wanderers vs chitipa kodi gayezi mukuti bwaji
"WISDINHO AKUYENERA KU FLAMES" - LIWEWE
Katswiri wonenera masewero a mpira wamiyendo, Steve Liwewe Banda, wati katswiri wa Mighty Mukuru Wanderers, Wisdom Mpinganjira akuyenera kupezeka ku Flames kamba ka kaseweredwe kake chaka chino.
Iye wayankhula izi kutsatira kuchita bwino kwa osewerayu chaka chino pomwe anasankhidwa kukhala osewera wapamwamba masewero a timuyi ndi Bullets loweruka latha.
Iye wati osewera ena omwe akutumikira Flames pakadali pano sangafikepo pa katswiriyu.
"Wisdom Mpinganjira akuyenera kupezeka ku Flames, iyeyu alibwino kuposa osewera ena alikutimuyi." Analemba chonchi Liwewe pa tsamba la Facebook.
Iye anayamikiranso mmene Wanderers inasewera mmasewerowa ndipo analangiza Bullets kuti akonze mavuto awo ngati akufuna ziyende.
Mpinganjira wasewera masewero onse chaka chino ndipo wasewera ngati wotseka kumbuyo chakumanja, kumanzere komanso mmbali.