"WISDINHO AKUYENERA KU FLAMES" - LIWEWE
Katswiri wonenera masewero a mpira wamiyendo, Steve Liwewe Banda, wati katswiri wa Mighty Mukuru Wanderers, Wisdom Mpinganjira akuyenera kupezeka ku Flames kamba ka kaseweredwe kake chaka chino.
Iye wayankhula izi kutsatira kuchita bwino kwa osewerayu chaka chino pomwe anasankhidwa kukhala osewera wapamwamba masewero a timuyi ndi Bullets loweruka latha.
Iye wati osewera ena omwe akutumikira Flames pakadali pano sangafikepo pa katswiriyu.
"Wisdom Mpinganjira akuyenera kupezeka ku Flames, iyeyu alibwino kuposa osewera ena alikutimuyi." Analemba chonchi Liwewe pa tsamba la Facebook.
Iye anayamikiranso mmene Wanderers inasewera mmasewerowa ndipo analangiza Bullets kuti akonze mavuto awo ngati akufuna ziyende.
Mpinganjira wasewera masewero onse chaka chino ndipo wasewera ngati wotseka kumbuyo chakumanja, kumanzere komanso mmbali.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores