"TIKHOZA KULANGA SULOM" - FAM YACHENJEZA
Bungwe la Football Association of Malawi lachenjeza bungwe la Super League of Malawi kuti lili ndi mphamvu zopereka zilango ku bungweli ngati angapitilize mchitidwe wosamvera komanso mwano kwa iwo.
Mu kalata yomwe yasainidwa ndi mlembi wamkulu, Alfred Gunda, yati bungweli likuchita ukamberembere wosamvera zina zomwe FAM inaika mmalamulo ake.
Iyo yati SULOM inachita zosemphana posaimitsa masewero a matimu omwe atumiza osewera odutsa atatu ku Flames pomwe akuti anasemphana ndi gawo 49 ya mmalamulo a SULOM. FAM yati SULOM ichotse masewero a matimuwa ndipo kupanda kutero, chilango chidzawatsatira.
Mabungwe awiriwa aonetsa kuchita zinthu mosagwirizana pomwe zaoneka masabata apitawa pomwe SULOM inakana kuchotsa masewero a Bullets ndi Wanderers pa bwalo la Kamuzu ndipo SULOM sinapereke ndalama za pakhomo ku FAM.
Matimu a Silver Strikers, Mighty Mukuru Wanderers komanso FCB Nyasa Big Bullets atumiza osewera anayi iliyonse ku Flames.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores