DE JONGH AKAYANKHA MLANDU KU SULOM
Bungwe la Super league of Malawi latsegulira mlandu timu ya Silver Strikers ndi mphunzitsi wawo, Peter De Jongh kamba kofuna kumenya oyimbira sabata yatha pomwe timuyi inalepherana 1-1 ndi Chitipa United pa bwalo la Civo.
Bungweli laika tsiku la lachiwiri pa 11 July 2023 ku Lilongwe hotel kuti akamve mlanduwu pomwe ayipeza ndi mbali ziwiri zoti ayankhepo monga:
•Kukanika kuteteza akuluakulu atimuyi ndi masapota pomwe analowa mbwalo la zamasewero.
•Kulowetsa masewero a mpira wamiyendo kukhala zipolowe.
Akapezeka olakwa, De Jongh ndi timu ya Silver alandira chilango kuchokera ku bungweli.
Akuyenela bas kulandila chilango mwina asinthako, zomwe anachita pamenepaja sizoyenela nkukhalanso couch wa timu yaikulu ngat imeneyi
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores